Iwo “Anaopa Mulungu Woona”
PAMENE Aisrayeli anali ku ukapolo ku Igupto, anamwino achihebri Sifra ndi Puwa anali m’mkhalidwe wovuta kwambiri. Poyesa kutsendereza mtundu wachilendowo kuti usachuluke, Farao analamula akazi amenewa kuti: “Pamene muchiza akazi a Ahebri . . . , akakhala mwana wamwamuna, mumuphe.”—Eksodo 1:15,16.
Sifra ndi Puwa “anaopa Mulungu [“woona” NW],” ndipo analimba mtima, chotero “sanachite monga mfumu ya Aigupto inawauza.” M’malomwake, analeka makanda aamuna akhale ndi moyo, ngakhale kuti kuchita zimenezo kukanawadzetsera mavuto. Yehova “anawachitira zabwino anamwino” amenewo, ndipo anawafupa chifukwa chopulumutsa miyoyo ya makandawo.—Eksodo 1:17-21.
Chochitikachi chikugogomeza kuti Yehova amayamikira awo amene akum’tumikira. Akanalingalira zomwe Sifra ndi Puwa anachita, kukhala kungosonyeza kukoma mtima kwaumunthu ngakhale kuti panafunika kulimba mtima. Ndi iko komwe, palibe mkazi woganiza bwino yemwe angalimbe mtima kupha makanda! Komabe Yehova mwachionekere anadziŵa kuti anthu achita nkhalwe yoipitsitsa chifukwa choopa munthu. Anadziŵa kuti anamwino amenewa sanasokhezereke ndi kukoma mtima kwaumunthu kokha ayi, koma kuti analinso oopa Mulungu komanso odzipereka kwa Iye.
Tili oyamikira zedi kutumikira Mulungu yemwe amaona kukhulupirika kwathu! Zoona, mwina palibe mmodzi yense wa ife amene chikhulupiriro chake chinayesedwapo monga mmene cha Sifra ndi Puwa chinayesedwera. Komabe, ngati sitikutekeseka pamene tikuchita choyenera—kaya kukhale kusukulu, kuntchito, kapena kwina kulikonse—Yehova samachiona mopepuka chikondi chokhulupirika chimenechi. M’malo mwake, ‘amabwezera mphotho iwo akum’funa iye.’ (Ahebri 11:6) Inde, “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”—Ahebri 6:10.