“Ulendo Wanga Wokacheza ku Nyumba ya Ufumu”
Laura,a wophunzira pakoleji ina, anapatsidwa ntchito yokakhala nawo pamapemphero a chipembedzo chilichonse ndi kulemba zomwe akazione. Iye anasankha Mboni za Yehova, ndipo chimangirizo chakecho anachipatsa mutu wakuti, “Ulendo Wanga Wokacheza ku Nyumba ya Ufumu.” N’kusiyana kwanji kumene Laura anakuona mwa Mboni? Zina mwa zochuluka zomwe iye anatchula ndi izi.
Ana: “Ana onse anali m’chipinda chimodzi ndi akuluakulu. M’matchalitchi onse momwe ndapitamo, ana amasiya makolo awo ndi kupita ku Sande Sukulu.”
Mgwirizano wa mafuko: “Nthaŵi zambiri, matchalitchi amakopa anthu a mtundu umodzi kapena fuko limodzi. . . . Koma Mboni za Yehova, zonse zinali kukhalira limodzi osati m’timagulu ta anthu ofanana m’njira ina yake.”
Mzimu wolandira alendo: “Anthu ambiri anadza kudzalakhula nane. . . . Ndipo ena anandifunsa ngati ndinali kuphunzira Baibulo ndi wina aliyense. Komabe, sindinadzimve kukhala wopanikizidwa. Iwo . . . anandilola kusankha chochita.”
Kunalibe wolandira zopereka: “Chinthu chimodzi chimene chinandidabwitsa kwambiri chinali chakuti panalibe munthu yemwe anali kulandira zopereka. . . . M’matchalitchi ena omwe ndakhala ndikupita, amalandira zopereka ngakhale m’makalasi a ana.”
Pali mipingo pafupifupi 90,000 ya Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi. Bwanji osakasonkhana nawo omwe uli pafupi ndi kwanuko?
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha dzina lake.