Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 12/1 tsamba 25
  • Kufutukuka kwa Teokalase M’Namibia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufutukuka kwa Teokalase M’Namibia
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko Limene Anatitumiza Kukachita Umishonale Linadzakhala Kwathu
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Baranaba ndi Paulo Ankathandiza Anthu Kukhala Ophunzira M’madera Akutali Kwambiri
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Nsanja ya Olonda—1999
w99 12/1 tsamba 25

Olengeza Ufumu Akusimba

Kufutukuka kwa Teokalase M’Namibia

UTHENGA wabwino wa Ufumu wa Mulungu unafika mu Namibia kwa nthaŵi yoyamba kumapeto a zaka za m’ma 1920. Kuchokera nthaŵi imeneyo, mazanamazana a anthu oona mtima alandira uthenga wa Mulungu wa chipulumutso. Zochitika zotsatirazi zikusonyeza momwe Yehova akusonkhanitsira zinthu zofunika zimenezi ku gulu lake.​—Hagai 2:7.

◻ Paulus, mlimi yemwe amakhala kumpoto cha kummaŵa kwa Namibia, anakumana ndi Mboni za Yehova kwanthaŵi yoyamba pamene anapita ku Windhoek, likulu la dzikolo. Mwamsanga Paulus anakhulupirira kuti wapezadi choonadi. Anabwerera kunyumba ali ndi buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Kenako, ali paulendo wopita ku Rundu, tauni yapafupi komwenso kunali Nyumba ya Ufumu, Paulus anakumana ndi Mboni ndipo anazipempha kuti zidzam’chezere.

Koma, komwe Paulus ankakhala kunali kutali kwambiri moti Mbonizo sizikanakwanitsa kumapita kumeneko kukachita naye phunziro la Baibulo mlungu ndi mlungu. Mosakhumudwa, Paulus anayamba kuphunzira Baibulo payekha. Kuwonjeza pamenepo, ankalalika zomwe ankaphunzirazo kwa ena mwakhama. M’kupita kwa nthaŵi, gulu la phunziro la Baibulo linakhazikitsidwa. Kagulu kameneka katamva pa wailesi kuti msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova udzachitikira ku Rundu, anasonkha limodzilimodzi pa zochepa zomwe anali nazozo ndi kulinganiza momwe adzayendere kuti akapezeke pa msonkhanowo.

Chinalitu chochitika chosangalatsa zedi kwa iwo, kukasonkhana ndi Mboni za Yehova kwa nthaŵi yoyamba! Pambuyo pake anapanga makonzedwe akuti abale oyeneretsedwa aziyendera gulu limeneli kaŵirikaŵiri. Lerolino, kuli ofalitsa asanu ndi mmodzi m’mudzi womwe Paulus amakhala.

◻ Chidwi cha Johanna pa dzina la Mulungu chinakula pamene iye anamva wina akunyoza Mboni za Yehova. Iye akukumbukira kuti: “Nditamva dzina lakuti Yehova kwa nthaŵi yoyamba, nthaŵi yomweyo linakhazikika m’malingaliro anga, ndipo ndinayamba kumadzifunsa kuti Yehova ndani. Ndinkakhala ndi mwamuna wanga pafupi ndi Walvis Bay pa gombe la Namibia. Nthaŵi ina tinapita kutauni, ndipo ndinaona Mboni zina zikugaŵira magazini a Nsanja ya Olonda m’msewu. Ndinalandira kope limodzi ndipo ndinapempha phunziro la Baibulo, popeza kuti ndinali ndi mafunso ambiri. Ndinalira pamene anandidziŵitsa kuti sanathe kubwera chifukwa chakuti galimoto lawo linali litawonongeka. Mosakhalitsa mwamuna wanga anamwalira, ndipo ndinasamukira ku Keetmanshoop. Mpainiya wapadera (mlaliki wanthaŵi zonse) anatumizidwa kudzagwira ntchito kumeneku, ndipo iye anandipatsa buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Kuchokera pachiyambi pomwe, ndinazindikira kuti chimenecho ndi choonadi.

“Kenako, anandiitana kuti ndizikagwira nawo ntchito yolalikira, koma ndinkachita mantha kwambiri ndi anthu. Pamene ndinali kuyenda khomo ndi khomo, ndinkapemphera kwa Yehova kuti kulibwino kuti ndingofa kusiyana n’kuti ndizilalikira. Pamene ndinakachita umboni wa mumsewu kwanthaŵi yoyamba, ndinabisala m’kanjira kakang’ono, kuti wina aliyense asandione. Pamapeto pake, ndinalimba mtima ndi kusonyeza magazini kwa yemwe ankadutsa, nthaŵi yomweyo ndinakhoza kunenapo kanthu. Ndi thandizo la Yehova, tsiku limenelo, ndinalankhula ndi anthu ambirimbiri za chiyembekezo changa chozikika pa Baibulo.

“Lerolino, pambuyo pa zaka 12, ngakhale kuti ndili wosauka mwakuthupi, ndausamalitsa mwayi wochita upainiya ndi kupitiriza kulandira chimwemwe chosaneneka kupyolera m’kugaŵana choonadi cha Ufumu ndi ena.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena