Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 12/1 tsamba 32
  • Kuyang’anizana ndi Mavuto a Kulera Ana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyang’anizana ndi Mavuto a Kulera Ana
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 12/1 tsamba 32

Kuyang’anizana ndi Mavuto a Kulera Ana

KULERA ana lerolino, makamaka azaka za unyamata, ndi vuto lalikulu zedi kwa makolo. Nyuzipepala ya The Gazette ya ku Montreal m’dziko la Canada, inati kumwa moŵa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo zangokhala “zizoloŵezi kwa achinyamata.” Nyuzipepalayi ikunenetsa kuti makolo ali ndi “udindo wokhala tcheru pa kusintha kwa khalidwe la achinyamata [awo].”

Kodi makolo ayenera kuonetsetsa mikhalidwe yotani yomwe ingasonyeze mavuto a achinyamata ameneŵa? Zizindikiro zina zochenjeza zoonekera mwakuthupi, m’malingaliro, ndi m’makhalidwe zotchulidwa ndi Sukulu ya ku America ya Ukatswiri wa Nthenda Zamaganizo a Ana ndi Achinyamata ndizo kukhala wofooka nthaŵi zonse, kusintha kwa umunthu ndi mkhalidwe, kudzitsekera kaŵirikaŵiri m’chipinda chogona, chizoloŵezi chochita makani, ndi kuloŵa m’vuto chifukwa chophwanya malamulo.

Kodi makolo angateteze motani ana awo ku mikhalidwe yovulaza imeneyo ndi zotsatira zake zoipa? Dr. Jeffrey L. Derevensky, wa pa Yunivesite ya McGill, akukhulupirira kuti kulankhulana momasuka ndi kupatsana ulemu ndi mwanayo m’zaka za kusinkhuka kwake kungachepetse mavuto m’tsogolo mwake. The Gazette inawonjezera kuti ngakhale kuli kwakuti chikhumbo chokhala ndi ufulu wowonjezeka chimaonekera pamene ayamba kusinkhuka, achinyamata amafunikabe “chitsogozo, chithandizo komanso chikondi cha makolo awo.” Ndemanga zimenezi zikugwirizana ndi mawu a m’mwambi wa m’Baibulo womwe umati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Mulungu akulangiza makolo kukhala zitsanzo, anzawo, wolankhulana nawo a ana awo, ndiponso aphunzitsi awo.​—Deuteronomo 6:6, 7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena