Anthu Kungokhala Nyama Zapamwamba?
“Kodi zili n’kanthu kuti timakhulupirira chiyani ponena za mmene moyo unayambira?”
Mtsikana wa zaka 16 zakubadwa wa ku Brazil anafunsa funso limeneli pamene anali kuyamba nkhani yake ya mutu wakuti “Anthu—Kungokhala Nyama Zapamwamba?” Mphunzitsiyu anauza mwana wasukulu ameneyu kuti alankhule kwa kalasi lonse pafunso limeneli atalandira kope la Galamukani wachingelezi wa June 22, 1998, lokhudza nkhaniyi.
Mboni yachinyamatayo inalongosola mmene chiphunzitso cha chisinthiko, chomwe ndi chozikidwa pa kusankha zamoyo zoyenera, chakhalira chowononga. Mwachitsanzo, anthu ambiri amakhulupirira kuti chiphunzitso cha chisinthiko chinachititsa ena kuona nkhondo ngati mbali imodzi ya kulimbana kosatha kwa amene ati akhale ndi moyo, zomwe zinathandiza kuyambika kwa Chifasizimu ndi Chinazi.
Wophunzirayu anasonyeza kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa anthu ndi nyama. Anafotokoza kuti: “Anthu okha angakule mwauzimu. Anthu okha ndiwo amafuna kudziŵa tanthauzo ndi cholinga cha moyo. Anthu okha ndiwo amavutitsidwa ndi imfa, amakhudzidwa ndi mmene moyo wawo unayambira, ndipo amakhala ndi chikhumbo chokhala ndi moyo kosatha. Kulitu kofunika kwambiri kuti tizithera nthaŵi yochulukirapo pa kufufuza zambiri ponena za gwero lathu!”
Mphunzitsiyo anatamanda nkhani yabwinoyo. Ananena kuti Mboni yachinyamatayo inalongosola bwino nkhaniyo chifukwa chakuti imakonda kuŵerenga. Kusukulu mtsikanayu amadziŵika kukhala woŵerenga wakhama wa zofalitsa zozikidwa pa Baibulo monga ngati Galamukani! ndi Nsanja ya Olonda.
Mboni za Yehova zili zokhudzidwa kwambiri ndi zimene chiphunzitso cha chisinthiko chikuchita mu mitima ndi m’maganizo a achinyamata. Pachifukwachi, mpingo umene kumasonkhana mtsikana ameneyu unalimbikitsa Mboni zachinyamata zonse kuti zigaŵire kope la Galamukani! wachingelezi wa June 22, 1998, kwa aziphunzitsi awo ndi anzawo akusukulu. Ndiye magazini okwana 230 anagaŵidwa m’masukulu osiyanasiyana mu mzindawo. Mkulu woyang’anira Dipatimenti ya Sayansi pasukulu ina analembetsa sabusikiripishoni ya Galamukani!
Inde, zimene timakhulupirira ponena za mmene moyo unayambira zilidi n’kanthu! Wachinyamata ameneyu pamodzi ndi anzake asonyeza kuti chikhulupiriro mwa Mlengi chimakhudzadi miyoyo yawo.