Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w00 4/1 tsamba 32
  • Mwambo Wapadera—Kodi Mudzakhalapo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwambo Wapadera—Kodi Mudzakhalapo?
  • Nsanja ya Olonda—2000
Nsanja ya Olonda—2000
w00 4/1 tsamba 32

Mwambo Wapadera​—Kodi Mudzakhalapo?

PATSIKU losaiŵalika zaka zoposa 3,500 zapitazo, Yehova Mulungu analamula banja lililonse la Aisrayeli ogwidwa ukapolo mu Igupto kupha mwana wa nkhosa kapena mbuzi ndi kuwaza magazi ake pamphuthu za nyumba zawo. Usiku womwewo, mngelo wa Mulungu anapyola nyumba zoikidwa chizindikiro mwanjira imeneyi koma anapha ana oyamba kubadwa m’nyumba za Aigupto onse. Pamenepo Aisrayeli anamasulidwa. Pokumbukira zimenezo, Ayuda anakhala akuchita phwando la Paskha.

Mwamsanga Yesu Kristu atamaliza kuchita phwando la Paskha wake wotsiriza pamodzi ndi atumwi ake, anayambitsa chakudya chimene chikakhala chikumbukiro cha imfa yake ya nsembe. Iye anapatsa atumwi ake mkate nanena kuti: “Tengani, idyani, ichi ndi thupi langa.” Ndiyeno anawapatsa chikho cha vinyo nati: “Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ndi kuchotsa machimo.” Yesu ananenanso kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Mateyu 26:26-28; Luka 22:19, 20) Chotero Yesu analamula otsatira ake kuchita mwambo wa imfa yake umenewu.

Chaka chino chikumbutso cha imfa ya Yesu chidzachitika Lachitatu, pa April 19, dzuŵa litaloŵa. Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zidzasonkhana pausiku wapadera umenewu kuchita nawo Chikumbutso monga momwe Yesu analamulira. Mukuitanidwa mwachikondi kudzakhala nafe monga oonerera. Chonde funsani Mboni za Yehova za kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yotsimikizirika ndi malo ake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena