Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w00 5/1 tsamba 32
  • Anafera Chikhulupiriro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anafera Chikhulupiriro
  • Nsanja ya Olonda—2000
Nsanja ya Olonda—2000
w00 5/1 tsamba 32

Anafera Chikhulupiriro

“TIMAKUMBUKIRA August Dickmann (yemwe anabadwa mu 1910), wa Mboni za Yehova.” Anayamba motero mawu olembedwa pa chikwangwani (chomwe chasonyezedwa pano) chomwe chinavundukulidwa posachedwapa ku Sachsenhausen, malo omwe kale anali msasa wachibalo. Koma n’chifukwa chiyani wa Mboni za Yehova akupezeka pa chikwangwani chotchuka chotere? Mbali yotsalayo ya chikwangwanichi ikufotokoza nkhani yonse kuti: “Anamuwombera ndi mfuti asilikali a SS pa September 15, 1939, chifukwa chokana kuchita zinthu motsutsana ndi chikumbumtima chake.”

August Dickmann anam’tsekera mu msasa wachibalo wa Sachsenhausen mu 1937. Patapita masiku atatu nkhondo yachiŵiri yadziko itayambika mu 1939 analamulidwa kusayina chikalata chokamenya nkhondo. Atakana, mkulu wa pa msasawo anam’neneza kwa Heinrich Himmler mkulu wa gulu la SS (Schutzstaffel, asilikali apadera a Hitler) komanso anapempha chilolezo kuti aphe Dickmann anthu onse okhala mu msasawo akuona. Pa September 17, 1939, nyuzipepala yotchedwa The New York Times inalengeza kuchokera ku Germany kuti: “August Dickmann, wazaka 29, . . . waphedwa ndi gulu lowombera ndi mfuti.” Nyuzipepalayo inatinso anali Mjeremani woyamba kukana kuchita motsutsana ndi chikumbumtima chake m’nthaŵi ya nkhondo imeneyo.

Patapita zaka 60, pa September 18, 1999, imfa ya Dickmann inakumbukiridwa ndi bungwe lotchedwa Brandenburg Memorial Foundation. Tsopano chikwangwanichi chimakumbutsa alendo za kulimba mtima ndi chikhulupiriro chake champhamvu. Chikwangwani chachiŵiri chomwe chili pachipupa chakunja kwa maloŵa omwe kale anali msasa wachibalo, chimakumbutsa alendo kuti Dickmann anali mmodzi wa Mboni za Yehova zokwana 900 zimene zinavutika m’ndende ya Sachsenhausen chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Anthu ena ambiri anavutikanso m’misasa ina. Inde, ngakhale nthaŵi zovuta ngati zimenezi zokhala m’misasa, ambiri anakhalabe okhulupirika pachikhulupiriro chawo kwa Mulungu.

Kwa Mboni za Yehova, ndi udindo wa Mkristu kuti “amvere maulamuliro [a boma] aakulu.” (Aroma 13:1) Komatu, pamene maboma akufuna kuwakakamiza kuti aphwanye malamulo a Mulungu, amatsatira chitsanzo cha atumwi a Kristu oyambirira, amene anati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Ndiyetu chifukwa chake m’dziko limene kudana kwa mitundu ndi mafuko kwapangitsa nkhanza zochititsa mantha, Mboni za Yehova kulikonse, mofanana ndi August Dickmann, zimalondola mtendere. Zimagwiritsa ntchito langizo la Baibulo lakuti: “Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.”​—Aroma 12:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena