Makolo Atsutsa Tsankho la Mphunzitsi
Mphunzitsi wa pasukulu ya pulaimale ku Cassano Murge, ku Italy, anapatsa ana asukulu ake timapepala tomata kuti atengere kunyumba kwawo. Timapepalato, timene anati akamate pa zitseko, tinali ndi mawu akuti: “Ndife Akatolika. Tikupempha Mboni za Yehova kuti zisagogode pano.”
Ena mwa makolo a anawo, ngakhale kuti si a Mboni za Yehova, anatsutsa mwamphamvu zimene anachita mphunzitsiyo. Malinga ndi kunena kwa magazini yotchedwa Muoviti Muoviti, makolowo anadzudzula mchitidwewo kuti, ‘kupatsa ana uthenga wotero kungawapangitse kukana aliyense amene saganiza mofanana nawo, kapenanso kupatula munthu chifukwa chosiyana “zipembedzo.”’ Ndiyetu mmodzi wa makolo amene analembera kalata kwa olemba magaziniyi anatchula kapepalako kukhala “mbewu ya namsongole, chipatso cha umbuli ndi kupusa.”
Ngati mmene lipoti limeneli likusonyezera, anthu ambiri a mitima yabwino amazindikira kuipa kwa kufesa mbiri ya tsankho. Amalemekezanso utumiki wachikristu wochitidwa ndi Mboni za Yehova mu Italy ndi kuzungulira dziko lonse lapansi. Bwanji osapempha Mboni za Yehova kuti zikuuzeni ‘chimene chili chiyembekezo chawo’? Adzakhala osangalala kukambirana nanu “mwaulemu.”—1 Petro 3:15.