Kukhalabe Okhulupirika kwa Yehova
KUKHULUPIRIKA kukusoŵa lerolino. Koma ngakhale zili tero, atumiki oona a Yehova Mulungu amadziŵika ndi mkhalidwe womwewo. Munthu wokhulupirika amakhala wolimba m’mayesero ndi wosabwerera m’mbuyo mosasamala kanthu za kupita kwa nthaŵi. Taganizani za Hezekiya amene anali Mfumu yabwino. “Atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye,” limatero Baibulo. N’chiyani chinam’siyanitsa Hezekiya ndi enawo? “Anaumirira Yehova,” ngakhale anali pakati pa olambira mulungu wonama Moleki. Inde, Hezekiya ‘sanapambuke pambuyo pa [Yehova], koma anasunga malamulo ake.’—2 Mafumu 18:1-6.
Munthu wina amene anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova anali mtumwi Paulo. Mbiri ya utumiki wake yopezeka m’Malemba Achigiriki Achikristu imachitira umboni wakuti Paulo analimbikira kutumikira Mulungu ndi moyo wake wonse. Poyandikira mapeto a moyo wake padziko lapansi, Paulo anadzinenera kuti: “Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro.”—2 Timoteo 4:7.
Komatu Hezekiya ndi Paulo anatiikira chitsanzo cha kukhulupirika chabwino bwanji! Titsanziretu chikhulupiriro chawo mwa kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu wathu Wamkulu, Yehova.—Ahebri 13:7.