Kodi N’kukhaliranji Wokhululuka?
“ASAYANSI akuchita kafukufuku amene wayamba kusonyeza kuti chikhululukiro chimaonjezeradi mtendere wa mumtima—ndiponso makamaka, thanzi lakuthupi,” inatero nyuzipepala yotchedwa The Toronto Star ya ku Canada. Komabe, Pulofesa Carl Thoresen wa pa Yunivesite ya Stanford, m’dziko la U.S.A., yemwe ndi wofufuza wamkulu wa Stanford Forgiveness Project, (Kafukufuku wa za Chikhululukiro pa Stanford) anafotokoza kuti pali “anthu ochepa kwambiri amene amadziŵa kuti chikhululukiro n’chiyani komanso mmene chimagwirira ntchito.”
Chikhululukiro chenicheni chimaonedwa kukhala mbali yofunika kwambiri ya Chikristu. Lipoti la The Toronto Star linatanthauzira chikhululukiro kukhala “kuzindikira kuti wina wakulakwira, kusiya kukhala ndi chakukhosi, ndipo pomalizira pake kuchita zinthu mwachifundo ngakhalenso mwachikondi ndi munthu wolakwayo.” Chikhululukiro chiyenera kusiyanitsidwa ndi kulekerera, kupeputsa, kuiŵala, kapena kukana cholakwa; komanso sichitanthauza kudziika mumkhalidwe wonyozedwa. Lipotilo linanena kuti chinsinsi cha chikhululukiro chenicheni ndicho “kupeŵa mkwiyo komanso malingaliro oipa.”
Ochita kafukufuku akuti, m’pofunika kupenda mosamala kwambiri mapindu akuthupi a kukhululuka. Komabe iwo akufotokoza za mapindu a m’maganizo, kudzanso “kusapsinjika maganizo kaŵirikaŵiri, kusada nkhaŵa kaŵirikaŵiri, ndi kusataya mtima kaŵirikaŵiri.”
Chifukwa chachikulu chokhalira wokhululuka chafotokozedwa pa Aefeso 4:32, pamene pamati: ‘Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.’ Pankhani ya chikhululukiro, monganso m’nkhani zina, tikulimbikitsidwa kukhala akutsanza a Mulungu.—Aefeso 5:1.
Kukana kukhululukira ena pamene tili ndi mwayi wa kuchitira chifundo kungawononge unansi wathu ndi Mulungu. Yehova amatiyembekezera kuti tizikhululukirana. Ndiyeno tingapemphere kuti atikhululukire.—Mateyu 6:14; Marko 11:25; 1 Yohane 4:11.