Kodi Ndinu Wozindikira?
POSANKHA oŵeruza a Israyeli, Mose anayesetsa kuti apeze amuna ‘ozindikira bwino, ndi odziŵika mwa mafuko awo.’ (Deuteronomo 1:13) Kudziŵa zinthu kumene kumabwera chifukwa cha kukula, si ndiko kunali cholinga chachikulu. Nzeru ndi kuzindikira zinali zofunikanso kwambiri.
Munthu amene ndi wozindikira amasonyeza kalankhulidwe kabwino pa zokamba ndi makhalidwe ake. Malinga n’kunena kwa dikishonale yotchedwa Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary, munthu wozindikira “amathanso kukhala chete mwanzeru.” Inde, pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;” ndipo munthu wozindikira amadziŵa kusiyana kwake. (Mlaliki 3:7) Kaŵirikaŵiri, pamakhala zifukwa zomveka zokhalira chete, n’chifukwa chake Baibulo limati: “Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.”—Miyambo 10:19.
Akristu amakhala osamala kuti akhale ozindikira pa zochita zawo ndi ena. Si kuti munthu amene amalankhula kaŵirikaŵiri kapena mwamphamvu ndiye amakhala wofunikira kapena wodalirika nthaŵi zonse ayi. Kumbukirani, Mose anali “wamphamvu m’mawu ake,” koma sakanatha kutsogolera moyenera mtundu wa ana a Israyeli kufikira atakulitsa mkhalidwe wa kuleza mtima, kufatsa, ndi kudziletsa. (Machitidwe 7:22) Mofananamo, awo amene aikizidwa udindo woyang’anira ena ayenera kumenyera nkhondo kuti akhale ofatsa ndi kusonyeza mzimu wololera.—Miyambo 11:2.
M’mawu a Mulungu, awo amene Yesu Kristu anawaikiza kukhala ‘oyang’anira zinthu zake zonse’ amatchedwa ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru [“wozindikira,” NW].’ (Mateyu 24:45-47) Iwo sachita zinthu mopupuluma mopitirira Yehova, kapenanso sazengereza kugwiritsa ntchito malangizo a Mulungu pamene amveketsedwa bwino pankhani ina. Amadziŵa nthaŵi yoyenera kulankhula ndi nthaŵi yoyenera kuyembekezera kuti aunikiridwe. Akristu onse amachita bwino potengera chikhulupiriro cha iwowo komanso pokhala ozindikira, monga momwe gulu la kapolo limachitira.—Ahebri 13:7.