Kodi Mgwirizano wa Zipembedzo Ukuoneka Kuti Ungatheke?
“Tili m’nthaŵi yofunika kwambiri m’mbiri ya matchalitchi athu,” anatero Christian Krause, pulezidenti wa tchalitchi cha Lutheran World Federation. Nayenso Papa Yohane Paulo Wachiŵiri analankhula za “mwambo wapadera pa ntchito yovuta ya kukhazikitsanso mgwirizano weniweni pakati pa Akristu.”
Ndemanga zolankhulidwa mosangalala kwambiri zimenezi, zinanenedwa chifukwa cha mwambo wosainira chikalata chachiyanjanitso chotchedwa Official Common Statement chimene chinasainidwa pa October 31, 1999, ku Augsburg m’dziko la Germany, chotsimikizira Mgwirizano pa Chiphunzitso cha Kukhululukidwa kwa Machimo. Tsiku ndi malo a mwambowu zinasankhidwa bwino ndithu. Akuti pa October 31, 1517, Martin Luther analemba mfundo 95 zofotokoza maganizo ake pankhani ya kukhululukidwa machimo ndipo anazikhoma pachitseko cha tchalitchi ku Wittenberg. Ichi chinali chiyambi cha matchalitchi achipulotesitanti. Inde, ku Augsburg komweko n’kumene anthu otsatira Martin Luther anapereka chikalata chosonyeza mfundo za chikhulupiriro chawo mu 1530, chotchedwa Chikhulupiriro cha ku Augsburg. Koma tchalitchi cha Katolika chinazikana mfundozo. Izi zinayambitsa kugaŵikana kosayanjanitsika pakati pa Chipulotesitanti ndi Chikatolika.
Kodi Chikalata cha Mgwirizano chimenechi chingakhale chodalirika pa kuthetsa kugaŵikana kwa tchalitchi, monga momwe chikunenera? Si mbali zonse zimene zinali kufuna kuti zinthu zikhale bwino. Akatswiri a maphunziro azachipembedzo 250 achipulotesitanti anasaina chikalata chokana Chikalata cha Chiyanjanitsocho, ndi kuchenjeza kuti asaponderezedwe ndi tchalitchi cha Katolika. Apulotesitantinso anakhumudwa pamene tchalitchi cha Katolika chinalengeza za kukhazikitsa chaka cha 2000 kuti chidzakhala chaka cha kukhululukidwa machimo kwapadera. Mchitidwe woterowu ndiwo umene unayambitsa kusiyana pakati pa mbali ziŵirizi zaka 500 zapitazo. Pakuti Chikhulupiriro cha ku Augsburg ndiponso kukanidwa kwake ndi tchalitchi cha Katolika kochitidwa pa Msonkhano wa ku Trent zikadagwirabe ntchito, n’zokayikitsa kuti mgwirizano ungatheke.
Kugaŵikana ndi kusagwirizana kwa Matchalitchi Achikristu ndi kwakukulu kwambiri kuposa zimene kusaina chikalata chilichonse cha mgwirizano kungakonze. Komanso, kukhala ogwirizana m’chikhulupiriro kumadalira kwambiri ziphunzitso za m’Mawu a Mulungu, Baibulo. (Aefeso 4:3-6) Mgwirizano weniweni umadza chifukwa cha kuphunzira ndi kuchita zimene Mulungu amafuna kwa ife, osati mwa kungololera. “Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.” Anatero mneneri wokhulupirika Mika.—Mika 4:5.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
© Ralph Orlowski/REUTERS/Archive Photos