Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w00 12/15 tsamba 32
  • “Chimene Aliyense Ayenera Kusangalala Nacho”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chimene Aliyense Ayenera Kusangalala Nacho”
  • Nsanja ya Olonda—2000
Nsanja ya Olonda—2000
w00 12/15 tsamba 32

“Chimene Aliyense Ayenera Kusangalala Nacho”

TUVALU, ndi dziko lokongola lopangidwa ndi zilumba zisanu ndi zinayi, zomwe zili m’nyanja ya South Pacific ndipo lili ndi anthu pafupifupi 10,500. Komabe, pozindikira kuti Mulungu “afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi,” Mboni za Yehova zakumeneko zinali kulakalaka zofalitsa zofotokoza Baibulo m’chinenero chawo. (1 Timoteo 2:4) Zimenezi zinali zovuta chifukwa chakuti panalibe dikishonale iliyonse ya chinenerocho. Mu 1979, mmishonale wa Mboni za Yehova yemwe akutumikira ku Tuvalu anagwira ntchito yovutayo. Iye ndi mkazi wake anali kukhala limodzi ndi banja la komweko ndipo anaphunzira chinenerocho. Pang’onopang’ono analemba mndandanda wa mawu a m’Chituvalu ndi matanthauzo ake. Pofika mu 1984, buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi linafalitsidwa m’Chituvalu ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Dr. T. Puapua, yemwe kale anali nduna yaikulu ya dziko la Tuvalu, analemba kalata yothokoza buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Analemba kuti: “Buku ili ndi chuma chatsopano ndiponso chapamwamba kuphatikiza pa ‘chuma’ cha mtengo wapatali cha Tuvalu. Muyenera kusangalala ndi ntchito imene mwagwira​—ntchito yapamwamba yokulitsa moyo wauzimu wa anthu a dziko lino. Ndikukhulupirira kuti ntchito imeneyi idzalembedwa m’mbiri ya Tuvalu pa mbali yosindikiza mabuku ophunzitsa. . . . [Ntchito] imeneyi ndi chinthu chimene aliyense ayenera kusangalala nacho.”

Mndandanda wa mawu amene wotembenuza ameneyu anasonkhanitsa ndiwo unakhala maziko a dikishonale ya Chituvalu kupita m’Chingelezi yomwe inasindikizidwa mu 1993. Imeneyi inali dikishonale yoyamba kwa anthu wamba m’chinenero chimenecho. Posachedwapa, bungwe loona za zinenero m’dzikolo la National Language Board of Tuvalu, linapempha chilolezo kuti ligwiritse ntchito mawuwo pokonza dikishonale yake yoyamba m’chinenerocho.

Kuyambira pa January 1, 1989, magazini ya Nsanja ya Olonda yakhala ikufalitsidwa m’Chituvalu kamodzi pamwezi. Ngati mukuŵerenga magazini ino m’chinenero chomwe si chanu, bwanji osayang’ana kuti muone ngati imafalitsidwanso m’chinenero chanu pa mndandanda wa zinenero za Nsanja ya Olonda patsamba 2? Mosakayikira, mudzakhala ndi chimwemwe chochuluka kuŵerenga magaziniyi m’chilankhulo chanu chenicheni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena