Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w03 7/1 tsamba 31
  • Vidiyo Imene Imakhudza Mitima ya Achinyamata

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Vidiyo Imene Imakhudza Mitima ya Achinyamata
  • Nsanja ya Olonda—2003
Nsanja ya Olonda—2003
w03 7/1 tsamba 31

Vidiyo Imene Imakhudza Mitima ya Achinyamata

ACHINYAMATA ambiri ataonera vidiyo yakuti Young People Ask​—How Can I Make Real Friends?a analimbikitsidwa kulingalira mofatsa khalidwe lawo. Vidiyoyi ili ndi malangizo opindulitsa a m’malemba, zimene Akristu achinyamata anena, ndiponso seŵero lolimbikitsa la makono lochokera pa nkhani ya m’Baibulo ya Dina. (Genesis, chaputala 34) Mawu onena za vidiyoyi otsatiraŵa anachokera ku Mexico.

Martha akuti: “Vidiyoyi inandikhudza mtima zedi. Ikuoneka ngati anapangira ine. Ndinkaganiza kuti popeza aphunzitsi anga ndi ana asukulu anzanga ankadziŵa kuti ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova, zimenezi zinali zokwanira. Ndinkalephera kusonyeza zimenezi mwa kuwalalikira. Ndimathokoza chifukwa cha nkhani zonse zimene Yehova amapereka, makamaka zikakhala zokhudza mtima ngati vidiyoyi.”

Juan Carlos anati: “Vidiyo imeneyi ndi yochititsa munthu kuganiza kwambiri. Monga wachinyamata, ndinachitapo zinthu zolakwa, ndipo ndinaona kuti zinali kufanana ndi za anthu ena a m’seŵeroli. Zaka zingapo zapitazo, ndinali ndi moyo wapaŵiri, koma ndinazindikira kuti moyo umenewu ukhoza kundipalamulira mavuto. Nditaonera vidiyoyi, ndinatsimikiza mtima kukhala wokhulupirika kwa Yehova.”

Sulem akuti: “Nditaonera vidiyoyi, inandikhudza mtima kwambiri. M’mbuyomo, ndinasiya kuŵerenga Baibulo, ndipo sindinali kupemphera kwa Yehova kwenikweni. Nditamva zimene achinyamata a m’vidiyoyi ananena, ndinalimbikitsidwa kuyambiranso kuŵerenga Baibulo ndi kupemphera kwa Yehova.”

Achinyamata ambiri masiku ano amakumana ndi mavuto ambiri, ndipo nthaŵi zambiri mabwenzi amene amasankha angakhudze kwambiri zimene amachita pamoyo wawo. (Salmo 26:4; Miyambo 13:20) Vidiyo yakuti Young People Ask​—How Can I Make Real Friends? ikuthandiza anthu ambiri kusankha mabwenzi mwanzeru.

[Mawu a M’munsi]

a Yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena