“Ndinapeza Mabwenzi, Chikondi, Ndiponso Kuganiziridwa”
“MWA ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Monga mmene Yesu ananenera, chikondi chinali chizindikiro cha ubale wa Akristu oyambirira. Tertullian, amene analemba buku lake patapita zaka zoposa 100 kuchokera pamene Kristu anafa, anagwira mawu anthu amene anaona zimene Akristu anali kuchita, kuti: ‘Taonani chikondi chimene ali nacho pakati pawo ndipo ndi okonzeka ngakhale kuferana.’
Kodi chikondi choterocho chingapezekenso m’dzikoli masiku ano? Inde. Mwachitsanzo, tamvani za kalata imene ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Brazil inalandira. Mkazi wina dzina lake Marília, amene analemba kalatayo anati:
“Pamene ndinali kukhala ku Villa Mercedes, ku Argentina, mayi anga omwe ndi m’modzi wa Mboni za Yehova, anadwala nyamakazi ya m’mafupa, imene inachititsa kuti apuwale ziwalo kuyambira m’chiuno kupita m’munsi. M’miyezi isanu ndi itatu yoyambirira imene anakhala akudwala, Mboni za ku Vila Mercedes n’zimene zinali kuwasamalira mwachikondi ndiponso zinali kuwaganizira. Mbonizo zinali kuchita chilichonse, kusesa ndi kukolopa m’nyumba mwawo ndiponso kuwakonzera chakudya. Ngakhale pamene anali kuchipatala, nthaŵi zonse panali munthu wina wowasamalira Mayiwo, usana ndi usiku.
“Ine ndi mayi tsopano tinabwerera ku Brazil, kumene akuchira pang’onopang’ono. Mboni za kumene tikukhala pakalipano zikuchita zonse zimene zingathe pothandiza kuti Mayi achire.”
Marília anamaliza kulemba kalata yake ndi mawu akuti: “Ine sindine Mboni, koma ndinapeza mabwenzi, chikondi, ndiponso kuganiziridwa pakati pa Mboni.”
Inde, alipobe anthu amene amasonyeza chikondi chenicheni chachikristu masiku ano. Pochita zimenezo, amasonyeza mphamvu imene zophunzitsa za Yesu zingakhale nazo pa moyo wathu.