Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w03 11/15 tsamba 32
  • M’tsogolomu Muli Dziko Lopanda Upandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • M’tsogolomu Muli Dziko Lopanda Upandu
  • Nsanja ya Olonda—2003
Nsanja ya Olonda—2003
w03 11/15 tsamba 32

M’tsogolomu Muli Dziko Lopanda Upandu

INGOYEREKEZERANI, ngati mungathe kutero, kuti padziko lonse palibenso apandu! Sipangafunikenso apolisi, ndende, kapenanso njira zopezera apandu ndi kuwalanga zomwe zimafuna ndalama zambiri komanso n’zovuta kwambiri. Lingakhale dziko lomwe aliyense akulemekeza moyo ndiponso katundu wa ena. Kodi izi zikumveka kuti n’zosatheka? Mungaganize choncho, komatu kusintha kochititsa chidwi kumeneku ndi komwe Baibulo limalonjeza. Bwanji osaona zomwe Malemba ananena pankhani ya upandu ndiponso zoipa zina zochitika padziko pano?

M’buku la Masalmo, timaŵerenga kuti: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:1, 2, 11) Kunena zoona, palibe munthu amene angalepheretse Mulungu kukwaniritsa lonjezoli ndiponso malonjezo ake ena onse osangalatsa kwambiri.

Mulungu adzadzetsa madalitso ameneŵa pogwiritsa ntchito Ufumu wake. M’pemphero la Ambuye, Yesu Kristu anaphunzitsa om’tsatira ake kupemphera kuti Ufumu umenewu udze ndiponso kuti chifuno cha Mulungu chichitike “monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Posachedwapa, mu Ufumu umenewu, padziko lapansi pano sipadzapezeka munthu aliyense wofuna kuchita zaupandu chifukwa cha umphaŵi, kuponderezedwa, kapena dyera. M’malomwake, Mawu a Mulungu amati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Salmo 72:16) Inde, Yehova Mulungu adzapatsa aliyense padziko pano zinthu zosatha. Chinthu chabwino kwambiri n’chakuti anthu azidzakonda Mulungu ndiponso anansi awo, ndipo dzikoli silidzasokonezedwanso ndi upandu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena