Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w04 5/1 tsamba 32
  • Kodi Mumalimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumalimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—2004
Nsanja ya Olonda—2004
w04 5/1 tsamba 32

Kodi Mumalimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu?

KODI mukakumana ndi mavuto mumalimbana nawo bwanji? Yesu anatha kulimbana ndi mayesero a Satana pokumbukira lemba loyenerera. (Mateyu 4:1-11) N’chimodzimodzinso ndi Mfumu Davide, itakumana ndi mavuto inalimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu. Davide anati: “Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.”​—Salmo 94:19.

Mofanana ndi zimenezi, kukumbukira lemba limene timalikonda kwambiri kungatitonthoze kapena kutilimbitsa tikakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, a Rex, amene panopa ali ndi zaka 89, akhala ali mlaliki wa nthaŵi zonse kuyambira mu 1931. Iwo anati: “Nthaŵi zambiri ndinkadziona kuti ndine wosayenerera ndikapatsidwa ntchito yapadera yoti ndichite mu utumiki.” Kodi anatani? “Ndinkakumbukira lemba limene ndimalikonda kwambiri, lemba la Miyambo 3:5, limene limati: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.’ Kukumbukira lemba limeneli ndi kuligwiritsa ntchito kunandithandiza kugwira ntchito yangayo bwinobwino.”

Ngakhale ana angapindule ngati akhala ndi lemba limene amalikonda kwambiri. Jack, wa zaka zisanu ndi chimodzi, anati lemba limene amalikonda kwambiri ndi Mateyu 24:14. Lemba limeneli limamulimbikitsa kupita kukalalikira ndi makolo ake. Iye anati: “Ndimakonda kupita kolalikira Loŵeruka lililonse pamodzi ndi mayi, bambo, ndi mchemwali wanga.”

Mofanana ndi Yesu, kodi nthaŵi zina mumakumana ndi mavuto oyesa chikhulupiriro chanu? Ngati ndi choncho, mwina lemba la Afilipi 4:13 lingakhale limodzi mwa malemba amene mungawakonde kwambiri. Kodi mumavutika ndi ‘malingaliro’ monga Mfumu Davide? Ndiye kuti kukumbukira lemba la Afilipi 4:6, 7 kungakuthandizeni kupirira. Kodi nthaŵi zina mumaganiza kuti kutumikira kwanu Mulungu kulibe phindu? Ngati ndi choncho, kukumbukira lemba la 1 Akorinto 15:58 kudzakulimbikitsani.

Mwa kuloŵeza pamtima malemba oyenerera, timalola kuti Mawu a Mulungu akhale ndi mphamvu m’moyo wathu. (Ahebri 4:12) Malemba omwe timawakondawo angatilimbikitse ndi kutitonthoza.​—Aroma 15:4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena