‘Funafunani Amene Ali Woyenera’
MZINDA wa Damasiko unali wotukuka m’zaka 100 zoyambirira Kristu Atabwera. Mzindawu unali pakati pa minda ya mitengo ya zipatso ndipo kwa magulu a anthu apaulendo ochokera kum’maŵa, anali malo amene ankapumulirako ulendo wawo. Pasanapite nthaŵi yaitali Yesu Kristu atamwalira, ku Damasiko kunakhazikitsidwa mpingo wachikristu. Ena mwa anthu a mumpingowo anali Ayuda amene mwina anakhala otsatira a Yesu pa Phwando la Pentekoste ku Yerusalemu m’chaka cha 33 Kristu Atabwera. (Machitidwe 2:5, 41) Ophunzira ena ochokera ku Yudeya ayenera kuti anasamukira ku Damasiko pamene chizunzo chinabuka, Stefano ataphedwa mochita kuponyedwa miyala.—Machitidwe 8:1.
Mwina m’chaka cha 34 Kristu Atabwera, Mkristu wochokera ku Damasiko dzina lake Hananiya anapatsidwa ntchito yodabwitsa kwambiri. Ambuye anamuuza kuti: “Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m’nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera.”—Machitidwe 9:11.
Khwalala lotchedwa Lolunjika linali lalitali pafupifupi kilomita imodzi ndi theka ndipo linkadutsa pakati pa mzinda wa Damasiko. Pachithunzi chochita kuzokota cha m’ma 1800 chimene chili patsamba linochi tingathe kuona mmene khwalalali linkaonekera kalelo. Tikaona mmene khwalalali analikonzera, n’kutheka kuti Hananiya zinam’tengera nthaŵi yaitali kuti apeze nyumba ya Yuda. Komabe, Hananiya anaipeza nyumbayi, ndipo ulendo wakewu unathandiza kuti Saulo adzafike pokhala mtumwi Paulo wolalikira uthenga wabwino mwakhama.—Machitidwe 9:12-19.
Yesu anali atatumiza ophunzira ake ndipo anali atawauza kuti ‘akafunefune amene anali woyenera’ uthenga wabwino. (Mateyu 10:11) Zikuoneka kuti Hananiya anachitadi kum’funafuna Saulo. A Mboni za Yehova ali ngati Hananiya chifukwa mosangalala, amafunafuna anthu oyenera ndipo amasangalala anthu akamalandira uthenga wabwino wa Ufumu. Kupeza anthu otere kumasonyeza kuti khama lawoli lapindula.—1 Akorinto 15:58.
[Chithunzi patsamba 32]
“Khwalala lotchedwa Lolunjika” panopa
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
From the book La Tierra Santa, Volume II, 1830