Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w05 6/15 tsamba 32
  • “Anazunzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Anazunzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake”
  • Nsanja ya Olonda—2005
Nsanja ya Olonda—2005
w05 6/15 tsamba 32

“Anazunzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake”

KU MALO ena ochezerako mu mzinda wa Cernobbio umene uli kumpoto kwa Italy, anakhazikitsa malo okumbukira anthu amene anawaphwanyira ufulu wawo wachibadwidwe. Chimodzi mwa zikwangwani zomwe zili pamalowa ndi cha Narciso Riet. Iye anabadwira ku Germany koma makolo ake anali a ku Italy. Anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova m’ma 1930. Nthawi imene Hitler anali kulamulira, Mboni za Yehova zinazunzidwa chifukwa chokana kuona Hitler monga woposa Mulungu woona, Yehova.

Pamene a Gestapo anadziwa kuti Riet anali kulowetsa magazini a Nsanja ya Olonda m’ndende zozunzirako, Iye anathawira ku Cernobbio. Ali kumeneko anapemphedwa kumasulira Nsanja ya Olonda m’chitaliyana ndi kuigawira kwa okhulupirira anzake omwe anali pafupi. Ntchito imene amachitayi inadziwika kwa asilikali. Msilikali wa SS ndi anthu ake analowa m’nyumba ya Riet ndipo anam’manga ndi kutenga mabaibulo awiri ndi makalata angapo, zomwe ankati ndi umboni wosonyeza kuti anaphwanya lamulo. Riet anatumizidwa ku Germany kumene anaikidwa m’ndende yozunzirako anthu ya Dachau. Iye anaphedwa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatsala pang’ono kutha. Iye “anazunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chake,” chinatero chikwangwani cha ku Cernobbio.

Chikhulupiriro cha Narciso Riet ndiponso cha Mboni zina zambiri zimene zinazunzidwa ndi a Nazi chimalimbikitsa Akristu masiku ano. Chimawathandiza kukhala okhulupirika kwa Yehova, amene ndi yekhayo m’chilengedwe chonse amene Mbonizi ziyenera kum’lambira. (Chivumbulutso 4:11) Yesu anati: “Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo.” Mulungu adzakumbukira ntchito zawo ndipo adzawapatsa mphoto chifukwa cha kulimba mtima kwawo.​—Mateyu 5:10; Ahebri 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena