Kodi Muli Ngati Mtengo wa Lagani Auna?
M’MUDZI wa kunja kwa Port Moresby, ku Papua New Guinea, atumiki awiri anali kupita kunyumba kuchokera muulaliki. Akuyenda, anaona mtengo wokongola. “Taonani, lagani auna,”anatero mwamuna wokulirapo pa awiriwo. Iye anayang’ana mwamuna wocheperapoyo, n’kupitiriza kulankhula kuti: “Dzina limenelo limatanthauza ‘mtengo wa chaka ndi chaka.’ Mosiyana ndi mitengo ina yambiri ya kumadera otentha, chaka chilichonse masamba a mtengowu amalakatika ndipo umaoneka ngati wakufa. Komabe, mvula ikagwa, umayambiranso kusangalala, kutulutsa maluwa, ndi kuonetsanso kukongola kwake.”
Mtengo wa lagani auna, kapena kuti mphampha, ungatiphunzitse kanthu kena. Malinga ndi zimene akatswiri ena amanena, mtengowu ndi umodzi mwa mitengo isanu yokongola kwambiri padziko lonse lapansi imene imatulutsa maluwa. Ngakhale kuti maluwa ndi masamba amalakatika nthawi ya chilimwe, mtengowu umasunga madzi. Mizu yake ndi yamphamvu ndipo imatha kumera mozungulira matanthwe amene amakhala pansi pa nthaka. Chifukwa cha zimenezi, mtengowu umalimba moti ngakhale mphepo yamphamvu singaugwetse. Mwachidule, tingati umakhala ndi moyo chifukwa chakuti umatha kupirira nthawi zovuta.
Mwina ifenso tingakumane ndi zinthu zimene zingayese chikhulupiriro chathu. Kodi chingatithandize n’chiyani kupirira? Mofanana ndi mtengo wa lagani auna, tingamwe ndi kusunga madzi opatsa moyo a Mawu a Mulungu. Tiyeneranso kugwiritsitsa zolimba ‘thanthwe lathu,’ Yehova, ndi gulu lake. (2 Samueli 22:3) Zoonadi, mtengo wa lagani auna ndi chikumbutso chochititsa chidwi chimene chingatithandize kusungabe mphamvu ndi kukongola kwathu kwauzimu ngakhale m’nthawi zovuta, ngati tigwiritsa ntchito thandizo limene Yehova amatipatsa. Tikatero, ‘tidzalowa malonjezo’ a Yehova, kuphatikizapo lonjezo la moyo wosatha.—Ahebri 6:12; Chivumbulutso 21:4.