Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w06 7/15 tsamba 32
  • “Kuyambira Lero, Ndakhulupirira Kuti Kuli Mulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kuyambira Lero, Ndakhulupirira Kuti Kuli Mulungu”
  • Nsanja ya Olonda—2006
Nsanja ya Olonda—2006
w06 7/15 tsamba 32

“Kuyambira Lero, Ndakhulupirira Kuti Kuli Mulungu”

MAYI wina wa ku Ukraine koma amene akukhala mu mzinda wa Prague, m’dziko la Czech Republic, dzina lake Alexandra, tsiku lina akuweruka kuntchito anatola kachikwama pamalo okwerera galimoto. Panthawi imene amatola kachikwamaka n’kuti anthu odutsa akungokapondaponda. Atakatsekula, sanathe kukhulupirira zimene anaona. Munali mpukutu wa ndalama za ma 5,000 koruna! Panalibe wina aliyense pamalopo amene ankaoneka kuti akufufuza kachikwamaka. Monga munthu wochita kubwera ku Czech Republic, sichinali chapafupi kuti Alexandra azidzipezera zosowa zake. Koma kodi pamenepa akanatani?

Atafika kunyumba, Alexandra anaonetsa mwana wake wamkazi, Victoria, kachikwama kaja. Onse awiri anafufuza m’kachikwamamo kuti mwina n’kupezamo dzina ndi adiresi ya mwini wake, koma sanapezemo chilichonse chokhudzana ndi zimenezi. Komabe, anangopezamo kapepala komwe kanali ndi manambala angapo ndithu. Mbali imodzi ya kapepalaka inali ndi nambala ya ku banki, mbali inayo inali ndi manambala enanso angapo. Anapezamonso mapepala ena onena za banki imene mwini wake amasungako ndalama komanso kapepala kena kolembedwa kuti ‘330, 000 koruna’ (pafupifupi madola 10,000 a ku United States). Zimenezi ndiye ndalama zonse zimene zinali m’kachikwama kaja.

Alexandra anayesetsa kuimbira foni bankiyo pogwiritsa ntchito manambala amene ankawaganizira kuti angakhale manambala a mafoni a ku banki, koma panalibe ngakhale imodzi yomwe inagwira. N’chifukwa chake Alexandra ndi mwana wake anaganiza zopita ku banki komweko n’kukafotokoza mmene zinakhalira. Abankiwo anapempha kuti awapatse nambala ya ku banki imene anapeza m’chikwamamo. Atafufuza pogwiritsa ntchito nambalayo, sanapeze aliyense amene anali ndi nambala ngati imeneyo. Tsiku lotsatira, Alexandra anapitanso ku bankiko ndi nambala ina imene anaipezanso m’chikwamamo. Eya! Apa m’pamene a banki anapeza kuti nambalayo inali ya mayi wina amene amasunga ndalama zake ku bankiyo. Alexandra ndi Victoria anaimbira mayiyo foni ndipo iye anavomereza kuti ndalamazo zinali zake. Potsirizira anakumana, ndipo mayiyo anawathokoza kwambiri. Pamenepa, iye anafunsa kuti, “Ndingapereke chiwongola dzanja chotani pa zimene mwandichitirazi?”

Victoria anayankha kuti: “Musapereke chiwongola dzanja chilichonse, tikadafuna zimenezo tikadangosunga ndalamazi.” M’chinenero chothyokathyoka cha m’dzikoli, Victoria anati: “Tikukubwezerani ndalamazi chifukwa chakuti ndife Mboni za Yehova. Timaphunzira Baibulo, n’chifukwa chake chikumbumtima chathu sichitilola kusunga zinthu zomwe sitinakhetsere thukuta.” (Ahebri 13:18) Ali wosangalala kwambiri, mayiyo anati, “Kuyambira lero, ndakhulupirira kuti kuli Mulungu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena