Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 4/15 tsamba 32
  • Zimene Adryana Analakalaka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Adryana Analakalaka
  • Nsanja ya Olonda—2007
Nsanja ya Olonda—2007
w07 4/15 tsamba 32

Zimene Adryana Analakalaka

MUMZINDA wa Tulsa, ku Oklahoma, m’dziko la United States, kuli kamtsikana kazaka 6 dzina lake Adryana. Kamtsikanaka kankalakalaka kwambiri chinthu chimodzi, chimene ndi chofanana ndi zimene Davide anatchula mu nyimbo yake, ponena kuti: “Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi: Kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’Kachisi wake.”​—Salmo 27:4.

Adryana ali ndi miyezi 6, anapezeka ndi khansa. Chifukwa cha matenda oopsawa, iye anapuwala miyendo. Madokotala anamupanga maopaleshoni ambirimbiri ndi kumupatsa mankhwala amphamvu kwambiri kwa chaka chonse.

Bambo ake a Adryana, amene si a Mboni za Yehova monga Adryana ndi mayi ake, anapempha bungwe linalake kuti litumize mwana wawo kumalo otchuka okasangalalako. Asanamutumize, a bungwelo anayamba afunsa Adryana. Iye anathokoza chifukwa chomuganizira koma anawauza kuti angakonde kukaona Beteli, likulu la Mboni za Yehova padziko lonse ku New York. Atamva zimene bambo ake anapempha, Adryana anapemphera kwa Yehova kuti apatsidwe mwayi wokaona Beteli. Ngakhale kuti poyamba a bungwelo anaona kuti Beteli singakhale malo abwino kwambiri kwa ana, iwo anamuloleza kupita bambo ake atagwirizana nazo.

Choncho, Adryana anapita ku New York kukaona Beteli pamodzi ndi mayi ake, mkulu wake, ndi mnzake. Adryana anati: “Yehova wamva pemphero langa. Ndinadziwa kuti atilola kupita ku Beteli. Kumeneko ndinaona mmene mabuku, magazini, ndi Mabaibulo amapangidwira. Ndinachita bwino kusapita ku malo okasangalala aja.”

Adryana ‘anapenyadi kukongola kwake kwa Yehova’ ndipo anayamikira kwambiri ntchito imene anaona yomwe imachitika pa likulu la anthu a Yehova. Inunso adzakulandirani mukapita ku Beteli. Kuwonjezera pa likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku New York, palinso maofesi a nthambi m’mayiko osiyanasiyana kumene mungapiteko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena