Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 6/15 tsamba 32
  • “Kodi Mulungu Mumamudziwa Dzina Lake?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Mulungu Mumamudziwa Dzina Lake?”
  • Nsanja ya Olonda—2007
Nsanja ya Olonda—2007
w07 6/15 tsamba 32

“Kodi Mulungu Mumamudziwa Dzina Lake?”

FUNSO limeneli linachititsa chidwi mayi wina kum’mwera chakumadzulo kwa Central Asia. Anaona funsoli pachikuto cha magazini yathu ya Galamukani! ya February 8, 2004. Mayiyu anatilembera kuti: “Nditangoiona magazini yanu, ndinachita nayo chidwi, ndipo inandithandiza kuganizira za mfundo za makhalidwe abwino. Tsopano ndayamba kuona kuti moyo wanga uli ndi cholinga. Ndimauza aliyense za Mulungu wathu ndiponso za mtendere umene munthu amapeza akadziwa Mulungu.”

Kumadera ambiri, “mpaka kumalekezero a dziko lapansi,” anthu ayamba kudziwa dzina la Mulungu lakuti Yehova. (Machitidwe 1:8) Mwachitsanzo, dzina limeneli m’Chitekimeni limalembedwa kuti Yehowa, ndipo limapezeka kwambiri m’Baibulo la Chitekimeni. Lemba la Salmo 8:1 limati: “Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!”

Pofuna kudziwa zambiri za Yehova Mulungu, mayi ameneyu anapempha kabuku kamasamba 32 kakuti Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha. Inunso mungapemphe kabuku kameneka kwa Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena