Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 11/1 tsamba 32
  • Kodi Mumagwiritsa Ntchito Mipata Youza Ena Chikhulupiriro Chanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumagwiritsa Ntchito Mipata Youza Ena Chikhulupiriro Chanu?
  • Nsanja ya Olonda—2007
Nsanja ya Olonda—2007
w07 11/1 tsamba 32

Kodi Mumagwiritsa Ntchito Mipata Youza Ena Chikhulupiriro Chanu?

M’DZIKO la Poland munali mpikisano wolemba chimangirizo pamutu wakuti: “Kodi choonadi chenicheni chilipo?” Mfundo zimene anthu anauzidwa kuti alembe m’chimangirizocho zinali zakuti: “Anthufe sitifunikira choonadi chenicheni. Palibe amene amafuna choonadi, ndiponso choonadi chenicheni sichingapezeke.” Mtsikana wina wazaka 15, dzina lake Agata, yemwe amaphunzira pa sukulu ina ya sekondale ndipo ndi wa Mboni za Yehova, anakonza zogwiritsa ntchito mpata umenewu kuti auze ena za chikhulupiriro chake.

Asanayambe kulemba chimangirizocho, Agata anapemphera kwa Yehova kuti amutsogolere. Kenako, anayamba kusonkhanitsa mabuku ndi magazini oti amuthandize polemba chimangirizocho. Iye anapeza mfundo zogwirizana ndi nkhaniyi mu Nsanja ya olonda ya July 1, 1995. Iye analemba funso limene Pontiyo Pilato anafunsa Yesu lakuti: “Choonadi n’chiyani?” (Yohane 18:38) Ndiyeno, iye analemba kuti funso limene Pilato anafunsa limasonyeza kuti ankakayika. Zikuoneka kuti Pilato ankafunsa kuti: ‘Choonadi? Choonadi n’chiyani? Kulibe choonadi!’ Ndiyeno, Agata analemba kuti: “Funso la Pilatoli likundikumbutsa mfundo zimene tauzidwa kuti tilembe m’chimangirizochi.”

Atatero, Agata anafotokoza za kufala kwa chikhulupiriro chakuti zimene munthu amakhulupirira kuti n’zoona sizingakhale zoona kwa munthu wina, koma onse angakhale akulondola. Ndiyeno, anafunsa mafunso monga akuti, “Ndani akanayerekeza kukwera ndege popanda kukhulupirira kuti malamulo a kayendedwe ka zinthu m’mlengalenga ndi oona?” Kenako, ponena za Baibulo iye anati: “Kuti munthu akhulupirire Mawu a Mulungu amafunika kukhala ndi umboni wotsimikizika.” Iye ananena kuti amakhulupirira kuti amene amayesetsa mwakhama kufufuza choonadi chenicheni amadekha mpaka atachipeza.

Agata anapatsidwa chikalata chaulemu ndipo anali ndi mwayi woti alankhule pamaso pa ophunzira ena onse a m’kalasi mwake. Anthu angapo pasukulupo anavomera kuti iye aziphunzira nawo Baibulo. Panopa, Agata akusangalala kuti anagwiritsa ntchito mpata umenewu kuti auze ena za chikhulupiriro chake. Kukhala wokonzeka kugwiritsa ntchito mpata womwe tingapeze kuti tiuze ena chikhulupiriro chathu kumakhala ndi zotsatira zabwino. Kodi inuyo mungagwiritse ntchito mpata uti kuti muuze ena chikhulupiriro chanu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena