Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 3/1 tsamba 32
  • Tsiku Lofunika Kwambiri M’mbiri Yonse ya Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsiku Lofunika Kwambiri M’mbiri Yonse ya Anthu
  • Nsanja ya Olonda—2009
Nsanja ya Olonda—2009
w09 3/1 tsamba 32

Tsiku Lofunika Kwambiri M’mbiri Yonse ya Anthu

Tsiku limeneli ndi tsiku limene Yesu Khristu anamwalira. N’chifukwa chiyani imfa ya Yesu inali yofunika kwambiri? Pali zifukwa zingapo.

Kukhulupirika kwa Yesu mpaka kufa kunasonyeza kuti munthu angathe kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu.

Imfa ya Khristu inapatsanso anthu ena mwayi wokalamulira naye kumwamba. Kuwonjezera apo, inatsegula njira yoti anthu ena ambiri adzasangalale ndi moyo wosatha m’paradaiso pa dziko lapansi.

Usiku woti mawa lake amwalira, Yesu anagwiritsa ntchito mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira monga zizindikiro za nsembe ya thupi lake yomwe anaipereka mwachikondi. Ndipo anauza ophunzira ake kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.” (Luka 22:19) Kodi inuyo mudzakumbukira nawo mwambo wofunika kwambiri umenewu?

Mboni za Yehova zikukuitanani kuti mukakhale nazo limodzi pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chaka chino tsiku la Chikumbutso chimenechi ndi Lachinayi, April 9, dzuwa litalowa. Mukhoza kudzapita ku Nyumba ya Ufumu yomwe muli nayo pafupi. Funsani a Mboni za Yehova kwanuko kuti mudziwe nthawi ndi malo ake enieni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena