Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 8/15 tsamba 23
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Ankakonda Mawu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Buku Limene “Limalankhula” Zinenero Zomwe Zilipo
    Buku la Anthu Onse
  • Khalani Achangu pa Nyumba ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Mukukumbukira?
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2009
w09 8/15 tsamba 23

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• Ngati mwana wabadwa wakufa, kodi pali chiyembekezo chakuti mwanayo adzauka?

Moyo wa munthu umayamba mayi akatenga pathupi. Yehova angathe kuukitsa munthu amene anamwalira pa msinkhu wina uliwonse chifukwa chakuti “zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.” (Maliko 10:27) Komabe Baibulo silinena ngati iye adzaukitsa ana amene anafa asanabadwe.​—4/15, masamba 12, 13.

• Kodi tingaphunzire chiyani kwa nyerere, mbira, dzombe ndi nalimata?

Zinthu zonsezi zimasonyeza kuti zili ndi nzeru zachibadwa. Motero, zimasonyeza kuti nzeru za Mulungu n’zosayerekezereka. (Miy. 30:24-28)​—4/15, masamba 16-19.

• Kodi ndi zochitika zapadera kwambiri ziti zokhudza Mboni za Yehova zimene zinachitika zaka 100 zapitazo, mu 1909?

Mu 1909, likulu la Watch Tower Bible and Tract Society, lomwe ndi bungwe la lamulo limene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito pofalitsa mabuku awo, linasamutsidwa kuchokera ku Pittsburgh, Pennsylvania, kupita ku Brooklyn, New York, kumene likugwirabe ntchito mpaka pano.​—5/1, masamba 22-24.

• N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti ndi bwino kukhala chete nthawi zina?

Baibulo limasonyeza kuti kukhala chete ndi umboni wakuti munthu ndi waulemu, wanzeru ndiponso wozindikira, komanso kumapatsa munthu mpata wosinkhasinkha. (Sal. 37:7; 63:6; Miy. 11:12)​—5/15, masamba 3-5.

• Kodi anthu awa: John Wycliffe, William Tyndale, Robert Morrison, ndi Adoniram Judson anachita zinthu ziti zofanana?

Anthu onsewa ankakonda Mawu a Mulungu ndipo anawamasulira m’zinenero zimene anthu wamba ankatha kuwerenga. Wycliffe ndi Tyndale anamasulira Baibulo m’Chingelezi, Morrison analimasulira m’Chitchaina ndipo Judson analimasulira m’Chibema (Chimyanima).​—6/1, masamba 8-11.

• Kodi ndi mafumu a Yuda angati amene anasonyeza changu kwambiri pa nyumba ya Mulungu?

Mafumu 19 ndi amene analamulira ufumu wakum’mwera wa Yuda. Koma anayi okha ndi amene anasonyeza changu chimenechi. Mafumu ake anali Asa, Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya.​—6/15, masamba 7-11.

• Kodi Mkhristu aliyense wodzozedwa amene ali padziko lapansi amakonza nawo chakudya chauzimu?

Ayi. Anthu onse odzozedwa ndi mzimu wa Mulungu amapanga gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, koma amene ali m’Bungwe Lolamulira ndi amene amayang’anira ntchito yopereka chakudya chauzimu.​—6/15, masamba 22-24.

• N’chifukwa chiyani asilikali achiroma anasirira malaya amkati a Yesu?

Pa nthawi imene Yesu anali kuphedwa, asilikali sanang’ambirane chovala chake. Popanga chovala chamtunduwu, anthu ankalumikiza nsalu ziwiri. Koma malaya a Yesu analibe msoko ndipo izi zinachititsa kuti akhale odula kwambiri ndiponso osowa.​—7/1, tsamba 22.

• Yesu anasiyana ndi atsogoleri achipembedzo pa kachitidwe kake ka zinthu ndi anthu. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikondi n’chimene chinamusiyanitsa kwambiri ndi iwo?

Atsogoleri achipembedzo sankakonda anthu wamba ndipo ankawanyoza. Ndiponso iwo sankakonda Mulungu. Yesu ankakonda Atate wake ndipo ankamvera chisoni anthu. (Mat. 9:36) Iye anali wachikondi, wachifundo komanso wokoma mtima.​—7/15, tsamba 15.

• N’chifukwa chiyani nkhani ya ndalama ingabweretse mavuto m’banja, ndipo n’chiyani chingathandize?

Nthawi zambiri kusiyana maganizo pa nkhani ya ndalama kumakhalapo chifukwa cha kusakhulupirirana kapena nkhawa imene wina amakhala nayo, komanso chifukwa chakuti anthuwo anakula mosiyana. Njira zinayi zimene zingathandize ndi izi: Muzikambirana modekha nkhani zokhudza ndalama, muziona kuti ndalama zimene mumapeza ndi za nonse, muzilemba bajeti ya banja ndipo muzigawana zochita.​—8/1, masamba 10-12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena