Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w12 6/1 tsamba 3
  • Kodi Baibulo Ndi Lofanana ndi Mabuku Ena?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Ndi Lofanana ndi Mabuku Ena?
  • Nsanja ya Olonda—2012
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Tonthozani Anthu Onse Olira’
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Tonthozani Amene ali ndi Chisoni
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Pezani Chitonthozo M’nyonga ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Mulungu Amatilimbikitsa Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2012
w12 6/1 tsamba 3

Kodi Baibulo Ndi Lofanana ndi Mabuku Ena?

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa . . .  kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.”​—2 TIMOTEYO 3:16, 17.

ANTHU ambiri sakhulupirira kuti mawu amenewa ndi oona. Kodi inuyo mumaona bwanji? Ponena za Baibulo, kodi ndi mfundo iti pa mfundo zotsatirazi imene mukugwirizana nayo?

• Ndi Buku limene linangolembedwa mwaluso basi

• Ndi limodzi mwa mabuku ambirimbiri amene ndi opatulika ndipo silisiyana ndi mabuku enawo

• Ndi buku la nkhani zakalekale koma zoti tingaphunzirepo kanthu

• Ndi Mawu a Mulungu

Funso lina lofunika kuliganizira ndi lakuti, kodi zimene timakhulupirira pa nkhaniyi zili ndi phindu lililonse? Taganizirani mawu awa, amene Baibulo limanena: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Pamenepatu Baibulo likunena kuti linalembedwa n’cholinga chakuti litilangize, kutilimbikitsa komanso kutipatsa chiyembekezo.

Komabe, Baibulo likanakhala kuti linangolembedwa bwino basi kapenanso likanakhala kuti ndi lofanana ndi mabuku ena onse achipembedzo, kodi mukanalikhulupirira kuti lingakulangizeni komanso kutsogolera banja lanu, makamaka zikanakhala kuti mfundo zake zikusiyana ndi zimene inuyo mumaona kuti n’zolondola? Ngati zimene zili m’Baibulo zili zabodza, kodi Baibulo lingakulimbikitseni komanso kukupatsani chiyembekezo choti zimene limalonjeza zidzakwaniritsidwadi?

Anthu ambiri amene amaphunzira Baibulo amakhulupirira kuti ndi buku lapadera komanso ndi Mawu a Mulungu. Kodi n’chifukwa chiyani iwo amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu? Kodi ndi zinthu ziti zimene zimasonyeza kuti Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi kuti muone zinthu zisanu zimene zimasonyeza kuti Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena