Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 10/1 tsamba 5
  • Mulungu Akonza Zopulumutsa Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Akonza Zopulumutsa Anthu
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Mesiya Ndiye Njira ya Mulungu Yopulumutsira Anthu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Tapeza Ife Mesiya”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Anthu Ankayembekezera Mesiya
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kufika kwa Mesiya
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 10/1 tsamba 5

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?

Mulungu Akonza Zopulumutsa Anthu

Mulungu analonjeza Abulahamu kuti “mbewu” ija idzakhala m’modzi mwa zidzukulu zake. Kudzera mwa mbewuyi, anthu a “mitundu yonse” adzadalitsidwa. (Genesis 22:18) Patapita nthawi, Yakobo, yemwe anali mdzukulu wa Abulahamu, anasamukira ku Iguputo komwe banja lake linakula n’kukhala mtundu wa Isiraeli.

Kenako, dziko la Iguputo linayamba kulamuliridwa ndi mfumu yankhanza, yomwe inkagwiritsa ntchito Aisiraeli ngati akapolo. Mulungu anasankha Mose kuti akhale mneneri ndipo anatsogolera mtundu wa Isiraeli kuchoka ku Iguputo kukadutsa pa Nyanja Yofiira, yomwe inagawika pakati mozizwitsa. Pambuyo pake, Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo, kuphatikizapo Malamulo Khumi, omwe ankawatsogolera komanso kuwatetezera. Malamulowo ankatchula nsembe zimene angapereke kuti akhulululukidwe machimo. Mulungu anauzanso Mose kuti auze Aisiraeli zoti adzawatumizira mneneri wina. Mneneriyo ndi amene anali “mbewu” yolonjezedwa ija.

Patapita zaka pafupifupi 500, Mulungu analonjeza mfumu Davide kuti “mbewu” imene inalonjezedwa m’munda wa Edeni idzalamulira ufumu womwe sudzatha. Mbewuyo idzakhala Mesiya, kapena kuti Mpulumutsi wosankhidwa ndi Mulungu, ndipo idzapulumutsa anthu onse ndi kubwezeretsa Paradaiso padziko lapansi.

Kudzera mwa Davide komanso aneneri ena, Mulungu anafotokoza zambiri zimene zikanathandiza anthu kuzindikira Mesiya. Analosera zoti Mesiya adzakhala wodzichepetsa ndi wachifundo ndiponso kuti muulamuliro wake simudzakhala njala, kupanda chilungamo komanso nkhondo. Anthu onse azidzakhala mwamtendere ndi anthu anzawo komanso ndi zinyama. Zinthu zonse zomwe sizinali mbali ya cholinga cha Mulungu zidzatha, monga matenda, mavuto komanso imfa ndipo anthu amene anamwalira adzauka.

Mulungu analosera kudzera mwa mneneri Mika kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu. Analoseranso kudzera mwa mneneri Danieli kuti adzachita kuphedwa ndiponso kuti Mulungu adzamuukitsa kwa akufa kenako n’kumuika monga Mfumu kumwamba. Danieli anadziwiratunso zoti Ufumu wa Mesiya udzalowa m’malo mwa maufumu onse a padziko lapansi ndipo udzalamulira mpaka kalekale. Koma kodi zimene analosera zokhudza Mesiya zinachitikadi?

​—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Genesis chaputala 22 mpaka 50; Ekisodo; Deuteronomo; 2 Samueli; Masalimo; Yesaya; Danieli; Mika; Zekariya 9:9.

DZINA LOYERA LA MULUNGU

Dzina la Mulungu lakuti Yehova limatchulidwa koyamba m’Baibulo pa Genesis 2:4. Dzina lapaderali limapezeka nthawi pafupifupi 7,000 m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. Zimene dzinali limatanthauza zimasonyeza kuti Mulungu angathe kukwaniritsa cholinga chilichonse chimene ali nacho ndiponso zimene walonjeza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena