Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 5/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Zinthu Zoipa Komanso Kuti Anthu Azivutika?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Zoipa Zizichitika Komanso Kuti Anthu Azivutika?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?
    Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?
  • N’chifukwa Chiyani Panopa Timakumana ndi Mavuto Ambiri?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 5/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi ndi ndani kwenikweni amene akulamulira dziko lapansili?

Zithunzi zosonyeza nkhondo, chiwawa, kusamvera malamulo ndi mavuto ena

Zikanakhala kuti Mulungu ndiye akulamulira dziko, kodi bwenzi padzikoli pali mavuto ambiri chonchi?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene akulamulira dziko lapansili. Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi? (Deuteronomo 32:4, 5) Baibulo limanena kuti dzikoli lili m’manja mwa winawake yemwe ndi woipa.—Werengani 1 Yohane 5:19.

Kodi zinatheka bwanji kuti woipayu azilamulira dzikoli? Anthu atangolengedwa, mngelo wina anapandukira Mulungu ndipo ananyengereranso mwamuna ndi mkazi oyamba kuti nawonso apandukire Mulungu. (Genesis 3:1-6) Anthu oyambirirawa anamvera Satana, zimene zinachititsa kuti akhale wolamulira wawo. Mulungu Wamphamvuyonse ndiye woyenera kulamulira. Komabe iye amafuna kuti anthu azisankha okha kulamulidwa ndi iyeyo chifukwa choti amamukonda. (Deuteronomo 6:6; 30:16, 19) Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amapusitsidwanso ngati mmene anthu oyambirira anachitira, potsatira zimene Satana ananena.—Werengani Chivumbulutso 12:9.

Kodi ndani adzathetse mavuto a anthu?

Kodi Mulungu alola kuti Satana azilamulirabe dzikoli mpaka kalekale? Ayi. Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu kuchotsa zoipa zonse zimene Satana akubweretsa padzikoli.—Werengani 1 Yohane 3:8.

Yesu adzawononga Satana pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa. (Aroma 16:20) Kenako, Mulungu adzayambanso kulamulira dziko lonse n’kupangitsa kuti anthu azikhala mwamtendere komanso mosangalala ngati mmene ankafunira poyamba.—Werengani Chivumbulutso 21:3-5.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 3 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena