Kodi Mungatani Munthu Yemwe Munkamukonda Akamwalira?
Na. 3 2016
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAGAZINI ya Nsanja ya Olonda imalemekeza Yehova Mulungu, yemwe ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu posachedwapa uchotsa zoipa zonse n’kusintha dziko lapansili kukhala paradaiso. Imalimbikitsa anthu kukhulupirira Yesu Khristu yemwe anatifera kuti tipeze moyo wosatha ndipo panopo akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Magaziniyi yakhala ikufalitsidwa kuyambira mu 1879 ndipo si yandale. Mfundo zake zimachokera m’Baibulo.
Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.
Ngati mukufuna kupereka ndalama zothandizira pa ntchito yolalikira pitani pa www.jw.org.
Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.