Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA OCTOBER 29, 2018–NOVEMBER 4, 2018
3 “Ngati Zimenezi Mukuzidziwa, Ndinu Odala Mukamazichita”
Zimene timadziwa sizingatithandize ngati sitimazigwiritsa ntchito. Koma tiyenera kukhala odzichepetsa kuti titsatire zimene timaphunzira. Nkhaniyi itilimbikitsa kutsanzira anthu odzichepetsa amene ankalalikira anthu amitundu yosiyanasiyana, ankapempherera ena komanso ankayembekezera Yehova kuti awathandize.
8 Akhristu Achikulire, Yehova Amayamikira Kukhulupirika Kwanu
MLUNGU WA NOVEMBER 5-11, 2018
12 Pitirizani Kusonyeza Chikondi Chifukwa Chimalimbikitsa
M’masiku ovutawa, tikhoza kupanikizika ndi mavuto. N’zoona kuti Yehova ndi Yesu amatithandiza kupirira mavuto. Koma tonse tiyeneranso kulimbikitsana. Nkhaniyi ikusonyeza zimene tingachite kuti tizilimbikitsana mwachikondi.
MLUNGU WA NOVEMBER 12-18, 2018
17 Anthu Amene Amatumikira “Mulungu Wachimwemwe” Amakhala Osangalala
Yehova ndi Mulungu wachimwemwe ndipo amafuna kuti atumiki ake azikhalanso osangalala. Koma kodi tingatani kuti tizikhala osangalala ngakhale tikukumana ndi mavuto m’dziko la Satanali? Mu ulaliki wake wapaphiri, Yesu anapereka malangizo amene angatithandize kukhala osangalala mpaka kalekale.
MLUNGU WA NOVEMBER 19-25, 2018
23 Yehova Ndi Wamphamvuyonse Koma Amaganizira Ena
MLUNGU WA NOVEMBER 26, 2018–DECEMBER 2, 2018
28 Tizikhala Okoma Mtima Komanso Oganizira Ena Ngati Yehova
M’dzikoli anthu ambiri ndi odzikonda koma Akhristu amadziwika kuti amakonda anthu. Munkhani ziwirizi tiona kuti iwo amasonyeza chikondichi pochita zinthu moganizira ena. Choyamba, tiona kuti Yehova ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yochita zinthu moganizira ena. Kenako tikambirana njira zina zimene tingamutsanzirire pa nkhaniyi.