Osaperekanso Mabuku pa Ngongole!
1 Panthaŵi ino, tili ndi mipingo yambiri imene ili ndi maakaunti oipa a mabuku kapena magazini. Oyang’anira dera asimba kuti kutenga mabuku pa ngongole ndiko chochititsa chimodzi cha maakaunti oipa a mipingo. Imeneyi ndi nkhani yodetsa nkhaŵa kwambiri m’munda wathu, chifukwa chakuti mipingo yambiri sikulandira mitokoma ya magazini ndi mabuku ogwiritsira ntchito iwo eni ndi muutumiki wakumunda.
2 Polingalira za mkhalidwewu womwe ukuchititsa mipingo yambiri kukhala ndi ngongole, tingakonde kulangiza mipingo yonse kusiya kupereka mabuku pa ngongole kwa ofalitsa. Ofalitsa ayenera kupereka kashi mofanana ndi apainiya. Motero, kuyambira tsopano kumka mtsogolo kakonzedwe kameneka kokana ngongole kadzagwira ntchito ponse paŵiri ku magazini ndi mabuku ndipo kwa apainiya ndi ofalitsa omwe. Tikhulupirira kuti kakonzedweka kadzathandiza mipingo kusamalira bwino maakaunti awo ndi Sosaite.