Lingalirani za Kukhala ndi Sabusikripishoni Yaumwini
1 Tidziŵa kuti kulandira kalata yachilimbikitso kuchokera kwa bwenzi lathu lapamtima kapena wachibale kumasangalatsa. Komabe, kodi ndi kuti kumene munthu angapeze chitonthozo chenicheni m’nthaŵi zovuta zino? Mosakayikira, ndi mwa kulandira ndi kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake, Galamukani!
2 Kodi Nsanja ya Olonda ili yofunika motani pa moyo wanu wauzimu? Kodi n’njofunika koposa? Ngati ndi choncho, mudzaiŵerenga mokhazikika chifukwa chakuti, monga mmene kwasimbidwira pa tsamba 2 ponena za chifuno chake, kope lililonse la Nsanja ya Olonda limaumirira ku Baibulo monga ulamuliro wake. Ndipo mungafune kuti ena, banja lanu, mabwenzi ndi anansi nawonso aziiŵerenga mokhazikika. Kupatulapo Baibulo, kodi mumadziŵa mabuku ena alionse amene amapatsa nzeru yaumulungu yochuluka yonga imene sabusikripishoni ya chaka ya Nsanja ya Olonda imachitira? Kodi inu mwininu munalembetsa sabusikripishoni? Kodi ziŵalo za banja lanu zinalembetsa sabusikripishoni? Pamene tili ndi sabusikripishoni, pamenepo tidzalandiradi kope lililonse la magazini ameneŵa, mwezi ndi mwezi.
3 Tidziŵa kuti Sosaite imagaŵira mabuku pa mtengo wotsika kutheketsa anthu kuwapeza. Mwezi uliwonse, anthu kaŵirikaŵiri amapatula ndalama zawo zosunga ndi zogulira zinthu ndipo zina za zinthu zimenezi ndi zamtengo kwambiri. Mofananamo, bwanji osapatulapo ndalama ya sabusikripishoni yaumwini? Magazini ameneŵa ali ndi ‘chakudya cha pa nthaŵi yake’ choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndipo chotero tifunikira kuwaika pa ndandanda yathu ya zinthu zofunika koposa.—Mat. 24:45-47.
4 Mwachitsanzo, kumadera akumidzi m’Malaŵi, kumene anthu ambiri amapeza zochirikiza moyo kupyolera mu ulimi, April ndi May ndi nthaŵi yakututa ndipo chotero ambiri angayembekezere kulandira ndalama zawo zapachaka za dzinthu dzawo panthaŵi imeneyi. Ngati muli mmodzi wa ameneŵa, bwanji osalingalira za kugwiritsira ntchito zina za ndalama zopezedwazo kulembetsa sabusikripishoni ya inu mwini ndi ya ziŵalo zina za banja lanu? Ndithudi, tonsefe tiyenera kulingalira za kukhala ndi sabusikripishoni yaumwini. Polembetsa sabusikripishoni, ndi bwino kugwiritsira ntchito keyala ya mpingo, ndiyeno Sosaite idzatumiza sabusikripishoni yanu mwa njira imodzimodziyo imene imatumizira mabuku ku mpingo wanu.
5 Ndithudi, mwa kulandira sabusikripishoni, mudzafupidwa ndi chidziŵitso ndi chilimbikitso chauzimu. Nazi zimene abale athu ena akumalo osiyanasiyana anena za phindu limene ofalitsa amene ali ndi sabusikripishoni yaumwini apeza: “Makolo anga sanali achuma, komabe ana anayi tonsefe tinali ndi masabusikripishoni athuathu. Nthaŵi zonse ndinaganiza kuti Sosaite inali kundidziŵa ine pa ndekha. Ngakhale pamene tinali tisanadziŵe kuŵerenga tinali ndi Nsanja ya Olonda yathuyathu.” “Ndikudziŵa banja lina limene chiŵalo chake chilichonse chimalandira kope laumwini mwa sabusikripishoni. Izo zimakonda kwambiri kuwaŵerenga ndipo zotsatirapo zabwino zimaonekera pamene awagaŵira pa makomo.”
6 Inde nkwabwino kuona kuti ambiri mwa ife timakhala ndi makope athuathu a Baibulo ndi makope athuathu a buku la nyimbo pamene tili pamsonkhano. Chotero bwanji osalakalakanso kukhala ndi sabusikripishoni yanuyanu? Mutangozindikira mapindu apadera a magazini athu aŵiriwo, mwachibadwa, mudzakhala wolembetsa sabusikripishoni wanthaŵi yonse.