Kuthandiza Achichepere Kupeŵa Zisonkhezero Zoipa
1 Kodi mumapeza kuti kukhutiritsa anthu achichepere kuyamikira phindu la Mawu a Yehova kungakhale kovuta? (Miy. 22:15) Kodi tingalimbikitse motani achichepere kupeŵa tsoka? Mtumwi Paulo anati: “Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda.” (1 Akor. 9:20) Mofananamo, kuthandiza achichepere kupeza ndi kuyamikira chitsogozo chauzimu chopindulitsa kumafunikira kuti mumvetsetse anthu achichepere ndi mavuto awo. Mpambo wa zamkatimu wa buku la Achichepere Akufunsa uli magwero abwino koposa a malingaliro a zimene mungalankhule. Mwa kuzoloŵera nkhani zimenezi, mudzakhala ndi chidziŵitso cha zimene anthu achichepere ambiri akulingalira lerolino.
2 Pamene mulankhula ndi wachichepere, nawu ulaliki wokhweka.
Pambuyo popatsana moni, sonyezani chithunzithunzi cha patsamba 105, ndi kufunsa kuti:
◼ “Kodi nchifukwa ninji zaka zauchichepere kaŵirikaŵiri zili magwero a nsautso yamaganizo? [Dikirani yankho.] Buku ili limakusonyezani mmene Baibulo lingathandizire anthu achichepere kulimbana ndi mikhalidwe yovuta, monga ngati imene yandandalikidwa pa zamkatimu.” Ndiyeno gaŵirani bukulo.
3 Mutadzidziŵikitsa, munganene kuti:
◼ “Ndili wosangalala kukhala ndi mwaŵi wakulankhula nanu chifukwa ndingakonde kumva lingaliro la munthu wachichepere. Mulungu amanena kenakake m’Baibulo kamene kalunjikitsidwa makamaka kwa anthu achichepere monga inuyo. [Ŵerengani Mlaliki 12:1.] Zikusonyeza kuti tiyenera kukumbukira Mulungu mu unyamata wathu ngati tikufuna mtsogolo mwachimwemwe. Kodi muganiza kuti muyenera kukhala wokondweretsedwa ndi Mulungu, Mlengi wanu? Kodi zimenezi zili ndi chiyambukiro chilichonse pa mtsogolo mwanu?” Dikirani yankho. Ndiyeno lunjikitsani chidwi ku lingaliro lofotokozedwa m’ndime 2 patsamba 319 la buku la Achichepere Akufunsa. Gaŵirani bukulo ndi kudzutsa funso lomwe mudzakambitsirana pa ulendo wanu wotsatira.
4 Kapena pambuyo popatsa moni mwininyumba, munganene kuti:
◼ “Makolo sangachinjirize kotheratu ana awo ku ziyambukiro zoipa. Koma kodi maganizo a mwana angalimbitsidwe motani? [Dikirani yankho.] Baibulo limatisonyeza mmene tingachitire. [Ŵerengani Aefeso 6:4.]” Ndiyeno mungapitirize, mukumanena kuti: “Buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza linalinganizidwira kuthandiza anthu achichepere. Limathandizanso makolo kukambitsirana ndi ana awo ponena za miyezo yabwino.”
5 Mayambidwe ena angakhale kusonyeza tsamba la zamkatimu la buku la “Achichepere Akufunsa” ndi kunena kuti:
◼ “Lerolino tikufunsa anansi athu kuti, Kodi muganiza kuti achichepere angapeze kuti mayankho oona mtima ndi othandiza a mafunso amene amafunsa, onga akuti: ‘Kodi mtsogolo mwandisungira chiyani?’” Dikirani yankho. Ndiyeno msonyezeni buku la Achichepere Akufunsa ndi kutchula kuti chinsinsi chenicheni cha chipambano cha bukuli chili m’chenicheni chakuti mayankho amene limapereka azikidwa, osati pa nthanthi kapena malingaliro a munthu mwini, koma pa choonadi chamuyaya chopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Perekani chogaŵira. Ngati mwininyumba atenga bukulo, sankhani mutu umene mungadzakambitsirane pa ulendo wanu wotsatira.
6 Yehova “safuna kuti ena aonongeke.” (2 Pet. 3:9) Zimenezi zimaphatikizapo achichepere. Komabe, anthu achichepere ambiri sadzapulumuka Armagedo. Lolani kuti zoyesayesa zathu za kulalikira mogwira mtima kwa achichepere zichititse chipulumutso kwa chiŵerengero chachikulu cha anthu achichepere, ku chitamando cha Yehova. Tiyenitu tithandizenso makolo kuona kufunika kwa kugwiritsira ntchito buku la Achichepere Akufunsa m’makambitsirano awo ndi ana awo.