Chikumbutso pa Kuchitira Lipoti Nthaŵi ya Utumiki Wakumunda Mochedwa ndi Molongosoka
M’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa December 1993, lipoti linasonyeza kutsika kwa maperesenti aŵiri mwa ofalitsa. Chotero tikukumbutsa ofalitsa onse kupitirizabe kugwiritsira ntchito malangizo operekedwa pa tsamba 4, ndime 5, ponena za malipoti ochedwa.
M’kope la Utumiki Wathu Waufumu wa June 1988, tsamba 5, zitsogozo zinaperekedwa ponena za kulemba lipoti la nthaŵi ya utumiki wathu wakumunda molongosoka. Patsamba 6, mfundo (h), kunatchulidwa kuti ‘ngati oposa anthu aŵiri apita pamodzi m’ntchito ya utumiki wa m’munda, kapena ngati oposa aŵiri apitira pamodzi kukachititsa phunziro la Baibulo, pamenepo aŵiri okha ndiwo angaŵerenge nthaŵi.’ Lingaliro limeneli la kugwira ntchito aŵiri aŵiri limapatsa aliyense mpata wa kugaŵana nthaŵi zonse m’kukambitsirana mbiri yabwino ndi anthu m’gawolo. Mwa njira imeneyi anthu ochuluka angafikiridwe kuposa pamene ofalitsa oposa aŵiri apitira pamodzi. (Luka 10:1) Komabe, timazindikira kuti pangakhale mikhalidwe pamene ofalitsa atatu apitira pamodzi ku phunziro la Baibulo. Sipangakhale choletsa kuti onse atatu aŵerenge nthaŵi. Komabe, tiyenera kukumbukira kuti, kwenikweni ali anthu aŵiri amene ayenera kuŵerenga nthaŵi paphunziro la Baibulo, koma mmodzi yekha ndiye amaŵerenga ulendo wobwereza ndi phunziro la Baibulo.
Monga momwe kwatchulidwira pamwambapa, pangakhale mikhalidwe imene ingalole anthu atatu kupita ku phunziro la Baibulo. Mikhalidwe yapadera yoteroyo ingakhale kumalo kumene kuli koopsa kwa wofalitsa kugwira ntchito ali yekha kapena ngati atsopano aŵiri satha kugwira ntchito m’gawo paokha angatsagane ndi wofalitsa wokhwima. M’zochitika zina, chifukwa cha mikhalidwe ya kumaloko, kungaoneke kukhala kosayenera kwa mbale kuyenda aŵiri ndi mlongo amene sali wachibale wapafupi. Motero, sitinaike lamulo losasintha lakuti ngati alipo atatu paphunziro, wachitatuyo sangaŵerenge nthaŵi. Kulingalira kwabwino kuyenera kugwiritsiridwa ntchito.