Zilengezo
◼ Chogaŵira cha July: Mabrosha akuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century. Mipingo imene idakali ndi timabuku tamasamba 32 m’sitoko iyenera kugaŵira timeneti m’munda. August: Lililonse la mabrosha amasamba 32 otsatirawa lingagwiritsiridwe ntchito: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano,” Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, ndi Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani? September: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Masabusikripishoni angagaŵiridwe pa maulendo obwereza. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene idzafuna zinthu za mkupiti zotchulidwa pamwambazi iyenera kuzioda pa Literature Order Form (S-14) yawo ya mwezi ndi mwezi yotsatira. Chonde musaode timabuku tamasamba 32, popeza kuti kulibeko ku Sosaite.
◼ Makonzedwe otsatirawa ayenera kupangidwa pa Maphunziro Abuku onse Ampingo mu mipingo imene ili yokhoza kupanga makonzedwe a kufika ku msonkhano wachigawo ukudzawo ku Zambia mlungu umenewo: Nkhani zophunziridwa zogaŵiridwa kaamba ka mlunguwo ziyenera kugaŵidwa paŵiri ndipo mbali yake imodzi iyenera kuphunziridwa pamodzi ndi nkhani zolinganizidwira mlungu wa msonkhano usanakhale pamene kuli kwakuti mbali yake inayo iyenera kuphatikizidwa ndi nkhani zolinganiziridwa mlungu wa pambuyo pa msonkhano wachigawo. Ngati nkotheka kuŵerengedwa kwa ndime kungasiyidwe. Mipingo ikukumbutsidwa kuti kuyesayesa kwapangidwa kwa kugaŵira masamba angapo okha pa mlungu kuti malemba onse opezeka m’phunziro logaŵiridwalo akaonedwe ndi kuŵerengedwa. Chilengezo chimenechi sichikukhudza mipingo imene sidzakhoza kufika pa msonkhanowo.
◼ Mtengo woyenera wa buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom ndiwo K40.00 kwa ofalitsa ndipo K30.00 kwa apainiya. Chonde ongolerani pa Mpambo wanu wa Mitengo wa April 1994.
◼ Zofalitsidwa Zomwe Zilipo:
Chingelezi: New World Translation of the Holy Scriptures—Reference Bible (Rbi8); Watch Tower Publications Index 1991-92; Watchtower Bound Volumes 1960-92.
◼ Makaseti Omwe Alipo:
Chicheŵa: Yehova Amapulumutsa Omwe Amaitanira pa Dzina Lake. Chingelezi: Doing What Is Right in Jehovah’s Eyes (seŵero latsopano); Yehova Amapulumutsa Omwe Amaitanira pa Dzina Lake; Jehovah’s Name To Be Declared in All the Earth; Kingdom Melodies No. 8.