Khalani ndi Mkhalidwe Wabwino Wamaganizo
1 Timakhala osangalala chotani nanga kuŵerenga za ziwonjezeko zabwino koposa zimene zikuchitika m’maiko ambiri! Komabe, tikuzindikira kuti m’madera ena ofalitsa Ufumu amakumana kaŵirikaŵiri ndi mphwayi, kusasamala, kapena ngakhale chitsutso chotheratu pa ntchito yathu yolalikira. Kodi tingakhale motani ndi mkhalidwe wabwino wamaganizo ngati zimenezi zimachitika m’gawo lathu? Kodi tingapeŵe motani mkhalidwe woipa wamaganizo umene ungatilande chimwemwe chathu kapena kuziralitsa changu chathu kaamba ka ntchito yopanga ophunzira?
2 Mkhalidwe wabwino wamaganizo udzatithandiza kukhala achikatikati. Ngakhale pansi pa mikhalidwe yopereka chiyeso, sitiyenera kulola maganizo oipa kulamulira kaonedwe kathu ka zinthu. Yesu anatiikira chitsanzo changwiro. Anthu ochepa kwambiri anavomereza zimene anaphunzitsa. Ambiri anakhumudwa ndi chiphunzitso chake. Iye anayang’anizana ndi mikhalidwe imene inayesa koposa chipiriro chake. Atsogoleri achipembedzo anasuliza ntchito yake ndi kupanga chiŵembu cha kumupha. Iye analavuliridwa, kuombedwa khofi, kusekedwa, kumenyedwa, ndipo potsirizira pake anaphedwa. Komabe, anapeza chimwemwe m’ntchito imene anali kuchita. Chifukwa ninji? Iye anazindikira kufunika kwa kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo sanaleme.—Yoh. 4:34; 13:17; Aheb. 12:2.
3 Khalani ndi Kaonedwe Kabwino ka Utumiki Wathu: Kuti tichite zimenezi, tiyenera kukumbukira mfundo zingapo. Kumbukirani kuti tili ndi uthenga umene anthu ochuluka amanyalanyaza kapena kutsutsa. (Mat. 13:14, 15) Ngakhale kuti atumwi analamulidwa mwalamulo kuleka kuphunzitsa m’dzina la Yesu, anakhalabe okhulupirika pa ntchito yawo yolalikira, ndipo zotuta zinapitiriza kudza. (Mac. 5:28, 29; 6:7) Timadziŵa pasadakhale kuti m’magawo ena, anthu oŵerengeka kwambiri adzamvetsera. (Mat. 7:14) Chifukwa chake, tili ndi chifukwa chakusangalala ngati munthu mmodzi yekha m’gawo lathu amvetsera. Kumbukiraninso kuti ngakhale awo amene amatsutsa ayenera kupatsidwa mwaŵi wakumva. (Ezek. 33:8) Otsutsa ena m’kupita kwa nthaŵi amasintha ndi kukhala olambira a Yehova. Pamenepo, pamene uonedwa moyenera, utumiki wathu umabweretsa lingaliro la chipambano, ngakhale ngati ochepa amvetsera. Kufika kwathu kwenikweniko pamakomo ndi uthenga wa Ufumu wa Mulungu kuli umboni.—Ezek. 2:4, 5.
4 Tili ndi chifukwa chabwino cha kukhalira ndi kaonedwe kabwino ka zinthu. Kupita patsogolo kwa ntchito yapadziko lonse ndi umboni wowonjezereka wa kuyandikira kwa chisautso chachikulu ziyenera kusonkhezera tonsefe kuchita zimene tingathe m’kutumikira mwa kudzipereka kwaumulungu. (2 Pet. 3:11, 14) Ntchito yachangu mu August idzakhala njira yabwino yosonyezera chiyamikiro chathu kaamba ka zimene tikuphunzira. Timafunanso kuti achatsopano asonyeze mkhalidwe wabwino wamaganizo kulinga ku kugwiritsira ntchito zimene akuphunzira. Ngati ena a ophunzira Baibulo athu apita patsogolo kufika pa kukhala okonzekera kukhala ofalitsa osabatizidwa, mwezi wa August ungakhale nthaŵi yabwino koposa ya kuwayambitsa.
5 Kaya tikutumikira monga ofalitsa kapena monga apainiya, tonsefe timathandizidwa ngati tikumbukira kuti zimene Yehova amafuna kwa ife sizolemetsa. (1 Yoh. 5:3) Iye amalonjeza kutichirikiza. (Aheb. 13:5b, 6) Mosasamala kanthu za kusasamala, mphwayi, kapena chitsutso cha anthu ochuluka, tiyenera kukhala otsimikiza ndi kupitiriza kulalikira chifukwa chili chifuniro cha Mulungu kuti tichite zimenezo.—1 Tim. 2:3, 4.