Kuphunzira Buku la Moyo Wanu wa Banja pa Phunziro Labuku Lampingo
1 Lerolino moyo wa banja uli pansi pa chitsenderezo. M’maiko ena anthu amafunsadi kuti, “Kodi banja lingapulumuke?” Buku la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe, limapereka malingaliro olunjika amene amathandiza kuthetsa mavuto ndi kupangitsa ukwati kukhala chinthu chosangalatsa chimene Mlengi anachilinganiza kukhala chotero.
2 Kukonzekera Ukwati Wachimwemwe: Yesu ananena choonadi chimene mbeta zingachigwiritsire ntchito: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?” (Luka 14:28) Inde, kuli kwanzeru kulingalira kaye ntchito yofuna kuchitidwa usanaiyambe. Zimenezo zili chimodzimodzinso ndi ukwati. Aphungu ambiri a ukwati amalangiza anthu awo kuti oyembekezera kukwatirana achite maphunziro, kapena apite kumalo okambitsirana za mavuto a m’banja, akumasintha mkhalidwe kuti ugwirizane ndi moyo wa muukwati ndi kulimbana ndi mavuto othekera. Phungu wina anati: “Ngati ana omaliza maphunziro kusekondale akanadziŵa zambiri ponena za ukwati monga momwe amadziŵira ponena za makompyuta, ukwati ukanakhala chinthu chokhutiritsa kwambiri.”
3 Mboni za Yehova zapereka chitsogozo chanzeru pambali imeneyi, chitsogozo chozikidwa, osati pamalingaliro a anthu amene amasinthasintha onena za zimene zimadzetsa chipambano m’moyo wa ukwati, koma pa uphungu wangwiro wa Woyambitsa wa ukwati. (Sal. 119:98-105) Nkhani zambiri zonena za ukwati zidzaphunziridwa pa Phunziro Labuku Lampingo, zimenezi zidzalola oyembekezera kuloŵa muukwati kumva ndemanga zothandiza kuchokera kwa amuna ndi akazi Achikristu amene ali ndi chidziŵitso chaumwini ndi amene ali ophunzira akhama a Mawu a Mulungu.
4 Ngati mukulinganiza kuloŵa muukwati, muyenera kulingalira mosamalitsa nkhani zofalitsidwa m’buku la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Lili ndi malangizo owonjezereka othandiza ochokera m’Mawu a Mulungu angwiro. Mitu ina njakuti “Kuyala Maziko Abwino a Ukwati Wanu,” “Pambuyo pa Tsiku la Phwando la Ukwati,” “Mwamuna Amene Amapeza Ulemu Waukulu,” “Mkazi Amene Ali Wokondedwa Kwambiri” ndi “Chikondi, ‘Chomangira Changwiro cha Umodzi.’” Linganizani kupenda nkhanizo ndi mnzanu wa muukwati wamtsogolo ukwati wanu usanakhale. Kukakhalanso kopindulitsa chotani nanga kwa inu kukambitsirana nkhanizo pamodzi ndi mbale amene ali Mkristu wokhwima maganizo amene mumalemekeza ndi amene angapereke malingaliro othandiza. (Miy. 4:1-9) Zimenezi zidzathandiza aŵiri nonsenu kusunga makonzedwe anu a phwando la ukwati loyembekezedwalo ali ogwirizana ndi zimene zili zofunika kwambiri, moyo wanu pokhalira limodzi monga anthu aŵiri okwatirana.
5 Konzekerani Kugwira Ntchito: Mwinamwake tingakhale titaona kuti ambiri amafika patsiku lawo la phwando la ukwati akumayembekezera kuti “padzachitika chinthu china chodabwitsa ndi chokondweretsa kwambiri pamene mungokwatirana.” Anthu okhala ndi lingaliro la maloto limeneli angagwiritsidwe mwala ndi chisoni. Choonadi nchakuti ukwati wachimwemwe ndi ntchito, ntchito yaikulu kuposa imene inachitidwa pa phwando la ukwati, mosasamala kanthu kuti linali lalikulu motani. Pa msonkhano wina wolangiza pa mavuto a muukwati wolinganizidwa ndi Profesa E. M. Pattison, mkazi wina wachichepere wotchedwa Betty anati: “Ndinali ndi maloto apadera ponena za ukwati, olimbikitsidwa ndi kuyembekezera kukhalira pamodzi. Komano panalibe chinthu chozizwitsa muukwati—kungogwira ntchito zolimba kokhakokha.”
6 Phunziro la Mawu a Mulungu liyenera kuthandiza kukonzekeretsa Akristu kuyang’anizana ndi zenizeni za moyo wa ukwati. Chifukwa ninji? Choyamba, chifukwa chakuti timadziŵa kuti anthu onse ali ndi choloŵa cha uchimo chochokera kwa Adamu. Aroma 3:23 amatitsimikizira kuti: “Pakuti onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” Motsimikizirikadi, munthu wosalungama amene ati akhale mnzanu wa muukwati adzakhala wopereŵera pa zinthu zina zimene mukuyembekezera. Pamene njira ya moyo wa tsiku ndi tsiku iyamba, mwamuna wanu angakhale wosaleza mtima, wofulumira kupsa mtima pang’ono, woonekera ngati waulesi kapena wonyalanyaza pang’ono mathayo ake a Malemba monga mutu wa banja lanu. Kapena, pamene mukhala ndi mkazi wanu, kuyandikirana kwapafupi kwa muukwati kungamsonyeze kukhala woonekera ngati wachabechabe, wolamulira, panthaŵi zina wosuliza kapena wokondetsa chuma.
7 Kukhala kwanu Akristu aŵiri nonsenu limodzi ndi chikhulupiriro mu uphungu wangwiro wa Mulungu kumapereka maziko owongolera zinthu. Mungakhoze kukambitsirana mwaluso komanso moona mtima ponena za mbali zimene aliyense angayamikire kuona kuti zikugwirizana ndi malangizo a Mulungu. Gwiritsirani ntchito nzeru ndi luntha posankha nthaŵi yokambitsirana nkhani zotero, osakambitsirana pamene wina wa muukwati ali woonekeratu kukhala wokhumudwa kapena wokwiya. Padzakhala zotulukapo zabwino koposa ngati, mkati mwa kukambitsiranako, muyesayesa mwakhama kupeŵa kutsutsa lingaliro la mnzanuyo. M’malo mwake, mvetserani kwenikweni ndi kuzindikira zimene akukana kapena zimene mnzanuyo akupempha.—Miy. 15:28; 18:13.
8 Kaŵirikaŵiri zimenezo zimachitika mwachibadwa pamene mwamuna ndi mkazi aphunzira phunziro lawo la banja la Malemba. Mkhalidwe weniweni wa makonzedwewo ungakhale wothandiza, pakuti umasonyeza mwamphamvu kuti onse aŵiriwo ali ndi chikhumbo choona cha kulandira uphungu wa Mulungu ndiponso chikhumbo cha kukondweretsana wina ndi mnzake. Chikhumbo cha m’Malemba chimenechi cha kukondweretsana wina ndi mnzake chimagwirizana ndi zimene mtumwi Paulo analemba kuti: “Yense payekha [amuna], yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziwopa mwamuna.”—Aef. 5:33; yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:4-7.
9 Makhalidwe Abwino Panyumba: Makhalidwe abwino a Mboni zachichepere kaŵirikaŵiri ali umboni wabwino kwambiri wa maphunziro amene mwachionekere amalandira panyumba. Ndithudi, makhalidwe athu ali chisonyezero cha moyo wathu. Kaamba ka chifukwa chimenechi, mosiyana ndi zimene ena angaganize, makhalidwe abwino ayenera kukhala ofunika panyumba. Ponena za zimenezi, monga momwe kulili m’mbali zina za moyo wa banja, chitsanzo cha makolo ndicho chinthu chofunika chachikulu. (2 Tim. 1:5) Kuuza ana kuti, “Chita zimene ndikunena, osati zimene ndikuchita” sinjira yowaphunzitsira makhalidwe konse. Zambiri zophatikizidwa m’makhalidwe abwino zimaphunziridwa, osati chabe ndi malangizo apakamwa, koma ndi kuona ndi kutsanzira. “Makolo sali aphunzitsi chabe; iwo alinso zitsanzo, pakuti ana athu amaphunzira mwa kutsanzira njira zathu,” akutero Beverley Feldman, wolemba Kids Who Succeed. Kodi ana anu amaona makhalidwe otani mwa inu?
10 “Atate inu, musakwiyitse ana anu” ndiwo uphungu wa Baibulo. (Aef. 6:4) Nkokhumudwitsa ndi kogwiritsa mwala kwa ana kuuzidwa kuti ayenera kukhala okoma mtima ndi olingalira ena, chikhalirechobe akumaona makolo awo akukangana, kudyera miseche ena, kuchita chipongwe, kapena kukwiya msanga. Kodi iwo angaimbidwe mlandu ngati achita m’mkhalidwe wofananawo? Kumbali ina, lembalo limapitiriza kunena kuti: “Komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Ndipo zimenezo zimaphatikizapo zofunika zoyambirira za makhalidwe abwino, zonga ngati kunena kuti, “Moni,” “Chonde,” “Zikomo,” ndi kuti “Pepani,” kusonyeza ulemu kwa anthu achikulire, ndi kugaŵana zinthu ndi ena. (Lev. 19:32; Aroma 16:3-7) Mikhalidwe imeneyi yophunziridwa panyumba paubwana idzakhala yothandiza kwa moyo wonse.—Miy. 22:6.
11 Chotero makolo ndi ana omwe ayenera kusonyeza makhalidwe abwino monga mbali yawo ya moyo wawo watsiku ndi tsiku m’malo mwa kuyembekezera kufikira panthaŵi ina yapadera. Pochita zimenezo, makolo ayenera kukhala oleza mtima ndi ololera zophophonya zimene ana angachite. Aloleni adziŵe kuti khalidwe lawo labwino nlofunika kwambiri kwa inu, ndipo khalani ofulumira kuyamikira kupita patsogolo kumene amachita. Zoonadi, zimenezi zimafuna kuyesayesa kwanu kochuluka. Koma kodi Malemba sananene kuti kuphunzitsa ana malamulo a mkhalidwe aumulungu kuyenera kuchitidwa “pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu”? (Deut. 6:7) Kuchita motero kumadzetsa mkhalidwe waubwenzi ndi wabwino panyumba, umene umathandiza kwambiri kulera ana anu pamene akukula kuti adzakhale achikulire othandiza, osamala ndi amakhalidwe abwino. Pamenepo adzabweretsa chitamando ndi ulemu kwa inu ndi kwa Mlengi wawo, Yehova Mulungu.
12 Kufesa Mooloŵa Manja mwa Kufika Pamisonkhano: Mtumwi Paulo pa 2 Akorinto 9:6 anati: “Iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa mooloŵa manja, mooloŵa manjanso adzatuta.” Mungafunse kuti: Kodi lamulo limeneli la kututa mooloŵa manja ngati tifesa mooloŵa manja limagwiranso ntchito pa kufika kwathu pamisonkhano yampingo? Ndithudi limatero! Tiyenera kumva monga momwe anachitira wamasalmo Davide pamene anati: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.” Inde, tiyenera kumva kukhala okakamizika kusonkhana ndi abale athu.—Sal. 122:1.
13 Kodi zimenezo zimafunanji kwa ife? Zimatanthauza kufika pamisonkhano yathu yamlungu ndi mlungu mokhazikika ndiponso mokhulupirika, ndiko kuti kuphatikizapo Phunziro Labuku Lampingo, osalola kachedwe kakunja koipa kapena kusamva bwino pang’ono m’thupi kukhala chodzikhululukira chokhalira kunyumba. Kodi ndi mwakaŵirikaŵiri chotani pamene timaona kunja kukhala kotentha kwambiri kapena kozizira, konyowa kapena kosaomba mphepo kukudodometsa kufika pamisonkhano? Komabe pamene tili ndi zopinga zowonjezereka zoti tigonjetse kuti tifike pamisonkhano, mpamenenso Yehova amaonekera kukhala akutipatsa dalitso lokulirapo. Zoonadi, kwa ambiri a ife, taŵerenga kale buku la Moyo Wanu wa Banja limene lidzaphunziridwa m’Maphunziro Abuku Ampingo. Motero, ena mwinamwake angaone mopepuka kufika pa phunziro la buku, akumalingalira kuti ngakhale ngati aphonya msonkhanowo, iwo amadziŵa kale nkhani zake. Komabe, pamene chaka chilichonse chikupyola, tingapeze kuti chidziŵitso cha m’buku limeneli chikukhala choyenerera kwambiri ndi chapanthaŵi yake kuposa mmene chinalili panthaŵi ina kumbuyoku. Tonsefe tifunikira kukhala maso ndi zochitika zamakono zimene zikupita patsogolo mofulumira pokwaniritsa ulosi wa Baibulo. Pamenepo tingakhale okonzekera kuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova. Pangani kukhala chonulirapo chanu kusaphonya msonkhano wa phunziro la buku uliwonse ngati kuli kotheka, mkati mwa nthaŵi imeneyi ya kuphunzira buku la Moyo Wanu wa Banja.
14 Kodi ndi m’njira zotani zimene tingayembekezere kututa mooloŵa manja m’zimenezi? Sitingathe kunena mawu olimbikitsa popanda kulimbikitsidwa ife eni; sitingathe kukondweretsa mtima wopsinjika wa wina popanda kukondweretsa mtima wa ife eni. Inde, sitingathe kupereka ndemanga momasuka pamisonkhano popanda kulimbitsa chikhulupiriro cha ife eni pa choonadi chimene timanena. Nzosavuta: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”—Miy. 11:25.
15 Phunziro Labuku Lampingo limatikonzekeretsa mu zambiri kuti tikhale aphunzitsi abwino kwambiri a Mawu a Mulungu. Komabe, kuti tikhale atumiki obala zipatso a Yehova Mulungu, tiyenera choyamba kufesa mooloŵa manja ponena za phunziro lathu laumwini la Baibulo. Tiyenera kufuna kukhala ndi njala yaikulu yauzimu, tikumazindikira kuti sitikhala ndi moyo ndi zinthu zakuthupi zokha. Pokhala ndi zofuna kusamaliridwa zonse ndi ntchito za moyo watsiku ndi tsiku zotitsendereza, kumafunikira kuyesayesa kosamala kuti tikhale ozindikira za chosoŵa chathu chauzimu. (Mat. 13:19) Kungakhaledi bwino kwambiri kwa ife eni kukhala ndi chiyamikiro cha Mawu a Mulungu chimene wamasalmo anali nacho pamene analemba kuti: “Ndikondwera nawo mawu anu, ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.”—Sal. 119:162.
16 Thandizo lotsimikizirika m’zimenezi ndilo kusamalira kwathu uphungu wa ‘kupenya bwino umo tiyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi.’ (Aef. 5:15, 16) Mwinamwake mungatofunikira kudzipenda pankhani imeneyi. Dzifunseni kuti: Kodi ndimalinganiza zochita zanga kotero kuti ndipeze nthaŵi ya phunziro la Baibulo laumwini kuphatikizapo kukonzekera misonkhano? Nthaŵi zina sitingakhale okhoza kupeza ola limodzi kapena aŵiri kuti tiŵerenge, komano mwa kukhala maso tingaombole mphindi zingapo apo ndi apo kuti tiŵerenge ndime zingapo m’buku loti liphunziridwelo. Akristu ambiri amalinganiza zodzuka mofulumirirapo ndi mphindi 10 kapena 15 tsiku lililonse kotero kuti aŵerenge pamene ali ogalamuka kwambiri. Ena amapeza kuti angathe kuŵerenga zambiri pamene akuyenda ulendo pa zoyendera za onse. Bwanji nanga za inu? Ngati tiŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimbirapo, chiyembekezo chabwinopo, ndi mkhalidwe wamaganizo wachimwemwe ndi wotsimikizirika. Ndiponso, tidzakhala okonzekeretsedwa bwino kwambiri kuchitira umboni kwa ena. Tidzakhala okhoza kuchirikiza makambitsirano abwino ndi kuthandiza abale athu pamene mipata ipezeka. Onani zimene zingakhale zotulukapo zake mu 1 Timoteo 4:15, 16.
17 Kufunika kwa Kukonzekera Bwino: Pokonzekera Phunziro Labuku Lampingo, kaya mukukonzekera nokha kapena ndi ziŵalo za banja, muyenera kukonzekera phunziro lanu bwino lomwe. Ŵerengani malemba oikidwa ndi kulingalira mmene akuchirikizira mafotokozedwe a nkhani imene ikuphunziridwayo. Mwanjira imeneyi mudzapindula zambiri koposa kungopeza mayankho a mafunso. Yesayesani kupeza osati chidziŵitso chabe komanso nzeru ndi luntha. (Miy. 4:7) Mbali ina imene muyenera kuchita ndiyo kukhala ndi phande mokwanira mwa kupereka ndemanga ndi kuŵerenga malemba. Pangani kukhala chonulirapo kuyankhapo mwinamwake kamodzi ndipo ngakhale nthaŵi zingapo pa phunziro lililonse. Kuchita motero kudzakuthandizani kusumika maganizo anu pa phunzirolo.
18 Kuti munthu apeze nzeru kuchokera m’chofalitsidwa chophunziridwa pa Phunziro Labuku Lampingo kumaphatikizapo zoposa kukonzekera, kufika pamsonkhanopo, ndi kukhala ndi phande. Kumatanthauzanso kuti ngakhale pambuyo pa phunzirolo, timapitirizabe ‘kusamalitsa zimenezi, ndi kukhalabe m’zimenezi.’ (1 Tim. 4:15) Ngati Mawu a Mulungu ati akhale nyali younikira m’mitima mwathu, tiyenera kuwalola kuyambukira munthu wamkatikati, zikhumbo, malingaliro, zisonkhezero, ndi zonulirapo zathu. (2 Pet. 1:19) Motero, tiyenera kudzifunsa ife eni mafunso onga akuti: Kodi chidziŵitso chimenechi chikutanthauzanji kwa ine pandekha? Kodi ndaphunziranji ponena za Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu? Kodi ndi malamulo amkhalidwe ati amene nkhaniyi ikugogomezera? Kodi ndikupeza lingaliro la phunziroli mu mtima mwanga? Kodi ndingagwiritsire ntchito motani choonadi chimenechi m’moyo wanga, m’banja langa, mu mpingo? Mwa kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira, tinganene monga momwe ananenera wamasalmo kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”—Sal. 119:105.