Tapatsidwa Zambiri—Zambiri Zikufunidwa kwa Ife
1 Ndife oyanjidwa kwambiri chotani nanga kukhala ndi choonadi! Chifukwa cha kudzipatulira kwathu kwa Yehova, ‘taikizidwa uthenga wabwino.’ (1 Ates. 2:4) Zimenezi zimatipatsa thayo lalikulu. Yesu anati: “Kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri.”—Luka 12:48b.
2 Ngoona chotani nanga mawu amenewo! Popeza kuti ife tonse tadala ndi chidziŵitso cha Mawu a Mulungu, mayanjano abwino kwambiri a abale, ndi chiyembekezo chabwino kwambiri, tinganenedi kuti tapatsidwa zambiri. Moyenerera, zambiri zikufunidwanso kwa ife.
3 Sungani Lingaliro Loyenera la Zofunika: Ena anena kuti zinthu zochulukitsitsa zikufunidwa kwa ife. Monga Mutu wa mpingo wachikristu, Yesu Kristu ndiye amene amasankha “zimene zili zofunika” kuti ugwire bwino ntchito. (Aef. 4:15, 16, NW) Amatitsimikizira kuti ‘goli lake lili lofeŵa, ndi katundu wake ali wopepuka.’ (Mat. 11:28-30) Iye amalolera mwachikondi awo amene ali opereŵera m’zinthu. (Luka 21:1-4) Ngati tipereka zabwino zathu zoposa, mosasamala kanthu za kuchuluka kwake, tidzadalitsidwa.—Akol. 3:23, 24.
4 Dzifunseni kuti, ‘Kodi zinthu za Ufumu nzoyamba m’moyo wanga? Kodi ndikugwiritsira ntchito nthaŵi ndi chuma changa mwanjira imene imatamanda dzina la Mulungu ndi kupindulitsa ena? Kodi ndimapeza kuti chikondwerero changa chachikulu chimadza m’kutumikira Yehova m’malo mwa kusangalala mwadyera ndi zinthu zakuthupi?’ Yankho lathu loona mtima kumafunso ameneŵa limavumbula zolinga za mitima yathu.—Luka 6:45.
5 Peŵani Kuyesedwa Kuchita Zimene Zili Zoipa: Ndi kale lonse sipanakhale ziyeso ndi zitsenderezo za kudzikondweretsa, umbombo, ndi kukonda chiwerewere zonga zomwe zilipo. Tsiku lililonse timayang’anizana ndi makhalidwe ovuta, ndi ziyeso kuti tigonje. Kuti tilimbane mwachipambano ndi zovuta zimenezi, tiyenera kupempha Yehova thandizo. (Mat. 26:41) Mwa mzimu wake, iyeyo angatilimbitse. (Yes. 40:29) Kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku ndiko thandizo lalikulu. (Sal. 1:2, 3) Kudzilanga ndi kudziletsa kumathandizanso kwambiri.—1 Akor. 9:27.
6 Kukonda chabwino sikokwanira—tiyeneranso kuda choipa. (Sal. 97:10) Zimenezi zimatanthauza kusakulitsa chikhumbo cha zinthu zimene zili zoipa. Miyambo 6:16-19 amandandalika zinthu zisanu ndi ziŵiri zimene Yehova amada. Mwachionekere, munthu amene amafuna kukondweretsa Yehova ayeneranso kuda zinthu zimenezo. Pokhala tili odala ndi chidziŵitso cholongosoka cha choonadi, tifunikira kuchita mogwirizana ndi chidziŵitso chimenecho, tikumasumika maganizo athu pa zinthu zabwino.
7 Kuli koyenerera kupempherera mikhalidwe imene ili yabwino kaamba ka “kuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse.” (1 Akor. 15:58) Ambiri apeza kuti kukhala ndi zochita zambiri mu utumiki wa Yehova kuli chitetezero chifukwa chakuti samakhala ndi nthaŵi ya kulondola zinthu zopanda pake.
8 Titalingalira zonse, zimene Yehova amafuna kwa ife nzochepa. (Mika 6:8) Tili ndi chifukwa chabwino chothokozera thayo lililonse la utumiki. (Aef. 5:20) Chotero, ‘timapitiriza kugwira ntchito zolimba ndi kuyesetsa,’ tili ndi chidaliro chakuti mfupo yathu idzakhaladi yaikulu koposa zilizonse zimene akufuna kwa ife.—1 Tim. 4:10.