Thandizani Achichepere Kuyamikira Buku Lakuti Achichepere Akufunsa
1 Nyengo ino yamakono yakhala yovuta kwambiri kwa achichepere ambiri. Kuwachititsa kuyamikira zinthu zauzimu nkovuta. M’mwezi wa March tidzakhala ndi mwaŵi wa kuthandiza achichepere mwa kugaŵira buku lakuti, Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Poligaŵira, tiyenera kukumbukira zimene zimakondweretsa achichepere ndi mavuto awo a kusukulu kapena a kumene amakhala kapena kumene amagwira ntchito. Chotero nchiyani chimene tinganene?
2 Njira yotsatirayi ingakhale yogwira mtima:
◼ “Kaŵirikaŵiri timaona unyamata kukhala nyengo yosangalatsa koposa m’moyo wathu. Koma, mwatsoka, timaona achichepere ambiri osakondwa lerolino. Si choncho kodi? [Yembekezani yankho.] Makhalidwe omasinthasintha achititsa dziko kukhala losokonezeka ndi la mavuto ambiri amene amayambukira achichepere ndi kuwalanda chimwemwe ndi chisangalalo. Kodi angapeze kuti chitsogozo chodalirika? [Yembekezani yankho.] Onani chimene Baibulo linena pa Salmo 119:9. [Ŵerengani ndi kukambapo.] Baibulo limasonyeza kuti thayo la kuphunzitsa chabwino nlamakolo ndiyeno limapereka chilangizo ichi pa Miyambo 1:8. [Ŵerengani.] Mogwirizana ndi zimenezi, buku lakuti Achichepere Akufunsa lili ndi chitsogozo chothandiza chochokera m’Baibulo, ndipo lili ndi zochitika zenizeni zambiri zimene zidzathandiza achichepere monga inu kudziŵa mmene mungayembekezere za mtsogolo ndi kukhala achimwemwe pochita zimenezo. [Sonyezani mitu ina imene mwasankha kuti mumkope chidwi.] Buku lothandiza la zithunzi zokongola limeneli lingakhale lanu pachopereka cha K1,200.00.”
3 Mwina funso lotsatirali lingabutse kukambitsirana kwabwino:
◼ “Kodi muganiza kuti chofunikira nchiyani kuti achichepere athandizidwe kulimbana ndi mavuto m’dzikoli? [Yembekezani yankho.] Baibulo limasonyeza kuti Mulungu akudziŵa mothetsera mavuto athu ndipo walonjeza kutithandiza. Kodi muganiza kuti kuphunzira Baibulo kungathandize achichepere kulimbana ndi mavuto? [Yembekezani yankho.] Bukuli likusonyeza mmene Baibulo lingathandizire achichepere kulimbana ndi mikhalidwe yovuta yonga iyi yondandalikidwa pa Zamkatimu.” [Tsegulani patsamba 8 ndi 9.] Ngati mwasankha kuti mukambitsirane nkhani ya chitsenderezo cha ausinkhu wa munthu, ŵerengani ndime 2 patsamba 78 ndi kufotokoza mmene Baibulo lingathandizire kuthetsa mavuto. Gaŵirani bukulo ndi kutchula chopereka chake.
4 Mwina kungakhale kosavuta kwa inu kunena zonga zotsatirazi:
◼ “Buku lakuti Achichepere Akufunsa nlapadera mwa njira zambiri. Lakonzedwa kuthandiza achichepere. Imodzi ya njirazo njakuti, limapereka chitsogozo cha makhalidwe chopeŵera tsoka kwa achichepere achibwana. (Mlal. 11:10) Zovuta zitabuka, ana amafunikira makolo osamala amene angawongolere kalingaliridwe ka ana awo. Chifukwa chake, bukuli limathandizanso makolo kukambitsirana ndi ana awo za miyezo yabwino. Bukuli limakopa maganizo anthu oona mtima, likumakulitsa chidwi pa Baibulo ndi chifuno cha Yehova.” Chotero tiyeni tonsefe tigwiritsire ntchito mwaŵi uliwonse kugaŵira bukuli m’gawo lathu.
5 Ngati mwininyumba ali wotanganitsidwa, mungamsiyire magazini kapena trakiti lakuti Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere. Mfunseni nthaŵi yabwino imene adzakhala womasuka. Mungatchule nkhani imene mufuna kudzakambitsirana kapena mungafunse funso. Zimenezi zidzachititsa mwininyumba kuyang’ana kutsogolo ku ulendo wanu wotsatira pamene funsolo lidzayankhidwa. Mutabwererako mukhoza kugaŵira buku.
6 Chidziŵitso chimene chili m’buku lakuti Achichepere Akufunsa chimakhudza achichepere onse. Chotero tiyeni tiwalimbikitse kuŵerenga chofalitsa chimenechi. Zoyesayesa zathu za kulalikira kwa achichepere mogwira mtima zipulumutsetu achichepere ochuluka kuloŵa m’dziko lapansi la paradaiso, ku chitamando cha Yehova.