Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/95 tsamba 5-6
  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 4/95 tsamba 5-6

Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa January 2 kufikira April 17, 1995. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Pamene Mulungu anavomereza kulapa kwa Davide chifukwa cha kuchimwa ndi Bateseba, Davide ndi banja lake anawonjoledwa ku ziyambukiro zoipa za khalidwe lake loipa. [14, uw-CN tsa. 127 ndime 5]

2. Lamulo la mkhalidwe logogomezeredwa pa Miyambo 11:1 nlakuti tiyenera kukhala ndi chikhalidwe chabwino cha mtima ndi oona mtima m’zochita zathu zonse za malonda ngati tikufuna chiyanjo cha Yehova. [12, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 11/15 tsa. 30.]

3. Kulandira uphungu ndiko chizindikiro cha kufooka. [13, uw-CN tsa. 127 ndime 4]

4. Miyambo 14:17 imapereka chisamaliro poyamba pa maganizo chifukwa chakuti kaŵirikaŵiri ndiwo amayambirira pasanakhale zochita. [13, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 8/15 mas. 20-1.]

5. Onse amene amatcha Yesu kukhala Ambuye adzapulumutsidwa. [2, uw-CN tsa. 105 ndime 5]

6. Mu 33 C.E., pamene anaukitsidwa ndi kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, Yesu anayamba kulamulira panthaŵiyo pa ophunzira ake odzozedwa. (Akol. 1:13) [10, gt-CN mutu 132]

7. Pafupifupi zaka 3,000 asayansi asanatulukire dongosolo la majini, Salmo 139:13-16 linasonyeza chidziŵitso cha ilo. [4, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 5/15 tsa. 4.]

8. Miyambo 8:22-31 ili malongosoledwe chabe a nzeru. [10, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 5/15 tsa. 28.]

9. Mkristu woona sayenera kuda kalikonse. [10, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 1/1 tsa. 21.]

10. Anthu asanu okha anaitanidwa ndi Yesu kuloŵa mkati kuti achitire umboni kuukitsidwa kwa mwana wamkazi mmodzi yekha wa Yairo. [10, gt-CN mutu 47]

Yankhani mafunso otsatirawa:

11. Kodi nkuyambira liti m’nthaŵi zamakono pamene anthu a Yehova anapatsidwa nyonga ya kupanga kuyesayesa kwapadera m’kulengeza mbiri yabwino? [5, om-CN tsa. 7]

12. Kodi ndani amene waika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuyang’anira utumiki lerolino? [6, om-CN tsa. 11]

13. Kodi kugonjera kwathu ku maboma adziko kumafika pati? [7, om-CN tsa. 15]

14. M’fanizo la Yesu la wofesa, kodi ndani amene akuphiphiritsiridwa ndi wofesa? [6, gt-CN mutu 43 ndime 23]

15. M’fanizo la Yesu la wofesa, kodi nchiyani chimene chikuphiphiritsiridwa ndi nthaka? [5, gt-CN mutu 43 ndime 15]

16. Kodi tingasonyeze motani m’zochita za tsiku ndi tsiku kuti tili ndi chikondi chodzimana kaamba ka abale athu? [16, uw-CN mas. 132-3 ndime 3, 4]

17. Kodi ndi chochitika cha m’mbiri chotani chimene Salmo 136:10-15 limasimba, ndipo nchiyani chinachitika kwa Farao? [3, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 6/15 tsa. 5.]

18. Kodi mwazi wokhetsedwa wa Kristu umatumikira zifuno ziŵiri ziti? [9, uw-CN tsa. 115 ndime 13]

19. Kodi Yairo anali yani? [9, gt-CN mutu 46]

20. Kodi nchifukwa ninji ophunzira a m’zaka za zana loyamba anaphunzitsa kuti Ufumu wayandikira, pamene 1914 inali idakali kutali kwambiri? [12, gt-CN mutu 49]

Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Ntchito yogwirizanitsa yotchulidwa pa Aefeso 1:9, 10 inayamba m’chaka cha ․․․․․․․ , [5, om-CN tsa. 5]

22. Mwa kunena kuti “Sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira” ․․․․․․․ anakhalabe ndi lingaliro lamphamvu la thayo pamaso pa Yehova la kulalikira mbiri yabwino kwa onse amene akamva. [6, om-CN tsa. 9]

23. Gulu la Yehova nlateokratiki, zimene zikutanthauza kuti ․․․․․․․; Yehova amapereka chitsogozo kudzera mwa Mu-tu wa mpingo, ․․․․․․․, kupyolera mwa Mawu Ake, ․․․․․․․; ndipo Yesu waikizira thayo lapadera kwa “ ․․․․․․․.” (Mat. 24:45) [10, uw-CN mas. 118-19 ndime 4-6]

24. Mosiyana ndi 144,000 amene akutengeredwa kumwamba, “ ․․․․․․․” limene palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, lidzapulumuka ․․․․․․․ pompano ․․․․․․․. (Chiv. 7:9, 14) [1, uw-CN tsa. 104 ndime 3, 4]

25. Pofuna kupanga chosankha chovomerezedwa ndi Mulungu, bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba linalingalira mosamalitsa zimene ․․․․․․․ ouziridwa ananena pa nkhani yokambitsiridwayo limodzinso ndi umboni wa kugwira ntchito kwa ․․․․․․․. (Mac. 15:6-29) [11, uw-CN tsa. 120 ndime 8]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Pamene alembi ndi Afarisi anapempha kuona chizindikiro kuchokera kwa Yesu, iye anawauza kuti “sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha (Yesaya; Malaki; Yona) mneneri.” [3, gt-CN mutu 42]

27. Kutsuka zovala zathu ndi kuziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa kumatanthauza kuti (taleka kuchita machimo; tazindikira kufunikira kwathu mtengo wansembe ya Yesu yotetezera machimo; tapatulira moyo wathu kwa Mulungu ndi kubatizidwa). [3, uw-CN tsa. 106 ndime 7]

28. Poyesa kusuliza zozizwitsa za Yesu, alembi ndi Afarisi anauza anthu kuti: “Uyu samatulutsa ziŵanda koma ndi mphamvu yake ya (mzimu woyera; Beelzebule; iyemwini).” [2, gt-CN mutu 41]

29. Atumiki onse okhulupirika a Mulungu amene anafa ndi kukhalabe akufa asanafike Pentekoste wa (36; 35; 33) C.E. sanadzozedwe ndi mzimu woyera kaamba ka moyo wakumwamba. [4, uw-CN tsa. 111 ndime 5]

30. Satana amatsutsa kuti anthu onse amasonkhezeredwa ndi (chikondi; chidani; chikhumbo chakupeza phindu laumwini) ndi kuti nkhaŵa yawo yaikulu ndiyo (dzina la Mulungu; ena; iwo eni). [12, uw-CN tsa. 124 ndime 14]

Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:

Miy. 3:27, 28; Yoh. 19:4-6; Miy. 15:5; Aroma 15:2, 3; Chiv. 7:16, 17

31. Chifukwa cha nkhaŵa yachikondi kaamba ka ana awo, makolo Achikristu amawapatsa zinthu zauzimu ndi zakuthupi zomwe. [15, uw-CN tsa. 131 ndime 14]

32. Timadera nkhaŵa kwenikweni ndi mmene maonekedwe athu amayambukirira ena, chotero mofunitsitsa timadzimana kudzikondweretsa. [15, uw-CN tsa. 130 ndime 10, 11]

33. Pamene tili ndi mwaŵi wakuchitira ena zabwino, kaya mwa njira yauzimu kapena yakuthupi, tiyenera kugwiritsira ntchito mpatawo ndi kuthandiza anthu anzathu, makamaka abale athu auzimu. [8, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 12/15 tsa. 20.]

34. Ulemu wodekha ndi bata poyang’anizana ndi nsautso zingadzetse ulemu kwa Yehova ndi kutipezera ulemu ndi anthu. [7, om-CN mutu 2]

35. Tayamba kale kusangalala ndi mikhalidwe yolonjezedwa imene moyenerera ingatchedwe “paradaiso wauzimu.” [3, uw-CN mas. 107-8 ndime 9-11]

S-97-CN-ZAM & MAL #285 4/95

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena