Kodi Mudzatamanda Yehova m’Nyimbo?
1 Nsanja ya Olonda ya May 1, 1994, masamba 8-13, inatithandiza kumvetsetsa mmene kuimba kunalili nkhani yaikulu m’nthaŵi za Baibulo. Inasonyeza mmene Mose ndi Aisrayeli ena onse anaimbira mwachilakiko atalanditsidwa ku gulu la nkhondo la Farao pa Nyanja Yofiira. Kunena zoona, kuimba kunali ndipo kukali ndi mbali yofunika pa kulambira kwathu Yehova. Chotero, tiyenera kuona kuimba kwathu nyimbo za Ufumu pamisonkhano yathu yosiyanasiyana kukhala nkhani yaikulu. Mipingo yonse ikulimbikitsidwa kukhala ndi programu yachikhalire ya kuphunzira nyimbo.
2 Kuti itithandize kukhala ndi phande kwambiri m’kuimba pa Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” ukudzawo, Sosaite yasankha nyimbo zotsatirazi zoti tidzaimbe: 3, 33, 38, 42, 45, 57, 61, 72, 85, 106, 107, 148, 152, 155, 183, 191, 200, 217.
3 Tikukulimbikitsani nonsenu, munthu aliyense payekha, mabanja ndi mipingo, kuyamba kuyeseza nyimbo zimenezi tsopano lino. Akulu angachite bwino kutsimikizira kuti nyimbozo zikuyesezedwa nthaŵi zonse. Malinga ndi ukulu wa chiyamikiro chathu kaamba ka makonzedwe a Yehova a msonkhano wa chaka chino, tidzamuimbira zitamando ndi moyo wathu wonse.