Kulitsani Chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu
1 Anthu ambiri amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Ena ambiri amakhulupirira mabuku ena otchedwa kuti mabuku opatulika. Palinso aja amene sadziŵa chimene angakhulupirire. Buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? nla anthu onse otero. Chofalitsa chimenechi chimasonyeza Baibulo monga mmene lilili. Chifuno cha bukuli ndicho kuthandiza anthu kuona kuti Baibulo lili Mawu a Mulungu. Limafotokoza ndi kutsutsa zinenezo zonama zambiri zoikidwa pa Mawu a Mulungu. Limapereka mayankho okhutiritsa pa mafunso ambiri. M’June, tidzakhala tikugaŵira buku labwino limeneli.
2 Anthu ambiri amene aŵerenga buku la Mawu a Mulungu avomereza kuti mafotokozedwe ake a Baibulo ngapadera. Mkazi wina ku United States of America amene anatchula kuti anali kufunafuna mtendere wa maganizo m’chipembedzo ananena zotsatirazi ataŵerenga bukulo: “Kufikira miyezi isanu ndi itatu yapitayo, ndinaganiza kuti sindidzaupeza. . . . Tsiku lina bwenzi langa limene lili Mboni linandipatsa buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Sindinasangalatsidwepo kwambiri ndi buku lina monga limeneli. Ilo lilidi limodzi la zofalitsa za Watch Tower Society zabwino koposa.” Kalata yochokera ku Buffalo, New York inati: “Ndangomaliza kumene kuŵerenga buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Silimangotchula mwatsatanetsatane kutsutsa Baibulo konse kwa munthu komanso limafotokoza bwino lomwe chifukwa chake ilo liyenera kulandiridwa monga Mawu a Mulungu.” Chotero tili ndi chidaliro chakuti enanso adzayamikira bukuli.
3 Mungasankhe kupereka ulaliki wachidule wonga uwu:
◼ “Tikukhala m’dziko lodzala mavuto ochuluka ndi njira zochepa kwambiri zowathetsera. Anthu omawonjezereka akumwerekera ndi anamgoneka. Anthu ambirimbiri nganjala. Mpweya umene tikupuma ndi madzi amene tikumwa zikuipitsidwa pang’onopang’ono. Panthaŵi imodzimodziyo, ambiri a ife timakumana ndi upandu. Kodi muganiza kuti mavuto onga ameneŵa adzathetsedwa konse? [Yembekezerani yankho.] Maumboni ochuluka amatsimikiza nkhani ya m’Baibulo yonena za Mlengi amene saali chabe wamphamvu kwambiri komanso amene amatikonda kwambiri.” Ŵerengani 2 Petro 3:13, ndi kufotokoza mwachidule kuti chili chifuno chake kuti dziko lapansi lidzale chilungamo.
4 Ngati mukufuna kufika pa mfundo msanga, munganene kuti:
◼ “Kodi munaganizapo za funso ili?” Sonyezani mutu, tsegulani patsamba 11, ŵerengani mafunso m’ndime 17, ndipo fotokozani kuti bukulo likupereka mayankho okhutiritsa.
5 Kapena mungayese zotsatirazi:
◼ “Kodi munayamba mwaganizapo kaya ngati sayansi yatsimikizira Baibulo kukhala lolakwika? Mwachitsanzo, asayansi ena amaumirira kuti dziko lapansi linakhalako mwa kuphulika kwakukulu kwa zinthu zakumwamba. Kodi muganiza bwanji? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu analenga dziko lapansi kukhala malo athu osatha. Nlosiyana ndi mapulaneti ena mu solar system yathu. Malinga ndi zimene tidziŵa, ndilo lokha m’chilengedwe chonse limene lili ndi zinthu zocholoŵana zofunikira kuchirikiza moyo.” Pitani pandime 6 patsamba 100 ndi kufotokoza chifukwa chake sayansi sinatsimikizire Baibulo kukhala lolakwika.
6 Njira ina ingakhale yofanana ndi iyi:
◼ “Anthu ena amaganiza kuti zozizwitsa zochitidwa ndi Yesu sizinachitike kwenikweni. Iwo amanena kuti zozizwitsa zimasemphana ndi malamulo achibadwa ndi kuti sizimachitika masiku ano. Kodi muganizapo bwanji?” Yembekezerani yankho. Sonyezani zimene zatchulidwa m’ndime 33 patsamba 86 ndiyeno ŵerengani Mateyu 19:26 kusonyeza kuti zozizwitsa zinachitikadi. “Bukuli limapenda maumboni ochuluka a m’Baibulo ndi akwina kusonyeza kuti Baibulo lili Mawu a Mulungu.” Tsegulani pampambo wa zamkati patsamba 3, ndi kusonyeza mitu ina yosangalatsa.
7 Bukuli lingakhale dalitso kwa anthu oona mtima amene anyengedwa ndi anthu opanda chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu. Umboni wamphamvu umene uli m’buku la Mawu a Mulungu ungathandize oterowo kukhala ndi chiyamikiro chachikulu kaamba ka Mlengi wathu, amene mwachikondi anatipatsa buku labwino koposalo.