“Lemekeza Yehova ndi Chuma Chako”
1 Mawu ameneŵa amafotokoza za kuchirikiza kwathu ntchito ya padziko lonse yolalikira. (Miy. 3:9) Kuwonjezera pa kukhala ndi phande mwachindunji m’ntchito ya kulalikira ndi kuphunzitsa, timalemekeza Yehova mwa kugwiritsira ntchito mwanzeru chuma chathu chakuthupi. Mwachitsanzo, mu Israyeli wakale pamene ndalama zinafunikira kaamba ka ntchito zapadera, monga ngati za kumanga chihema ndipo pambuyo pake za kachisi, chilengezo chachidule chinaperekedwa ndipo anthu anapereka mowoloŵa manja kwakuti nthaŵi zina anapereka “zoposa zimene zinafunika.” Timakumbutsidwanso za mmene Yesu ndi ophunzira ake analili ndi thumba la ndalama kapena bokosi la onse limene anali kutengamo ndalama zothandizira osauka ndi kugulira zinthu zina zofunika.—Eks. 36:5-7, NW.
2 Lerolino, Mboni za Yehova zikupitiriza kutsatira njira zakale zimenezi za kugwira ntchito zolimba ndi kupereka mowoloŵa manja. Chifukwa chake, mpingo uliwonse uli ndi mabokosi a zopereka, amene kaŵirikaŵiri amaikidwa kumbuyo kwa Nyumba Yaufumu ndi kulembedwa moonekera bwino kuti—za Ntchito ya Padziko Lonse ya Sosaite, Ndalama za Sosaite za Nyumba Zaufumu, ndi ndalama za zosoŵa za mpingo. Ndi bwinonso kuti mabokosi a zopereka aikidwe m’malo a phunziro labuku osiyanasiyana. Ndalama zolandiridwa pa Nyumba Yaufumu ndi m’malo ameneŵa zimagwiritsiridwa ntchito kugulira zofunika za Nyumba Yaufumu kapena kuchirikizira zinthu za Ufumu monga momwe mpingowo ungasankhire. Kodi mpingo wanu uli ndi mabokosi azopereka otero amene munthu aliyense angaikemo ndalama zilizonse zimene akufuna popanda kuumirizidwa kapena kukakamizidwa?—2 Maf. 12:9, 10; Luka 21:1.
3 Ndiponso, pali ndalama za Sosaite za mabuku ndi magazini zimene mpingo umasunga kupyolera mwa mkulu kapena mtumiki wotumikira wosankhidwa ndi bungwe la akulu. Mwatsoka, mipingo ina yakhala isakusunga bwino zolembapo zawo, zikumachititsa maakaunti oipa a mabuku ndi magazini. Chotero, mfundo zimene zili m’mafunso ndi mayankho otsatirapowa zidzakhaladi zothandiza:
◼ Pambuyo pa msonkhano uliwonse, abale aŵiri ayenera kutsegula bokosi la zopereka ndi kuŵerenga ndalama zake. Kodi nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika?
Njira imeneyi imachititsa onse kutsimikizira kuti ndalama zoperekedwazo zikusamaliridwa bwino. Tiyenera kukhala ndi nkhaŵa yofanana ndi imene Paulo anali nayo posamalira “chopereka chaufulu” chimene chinaperekedwa ndi mipingo kuti athandize abale a ku Yudeya. Onani nkhani yolembedwa pa 2 Akorinto 8:19-21, NW. M’vesi 19 Paulo ananena za Tito amene anasankhidwa kuyenda naye ulendo “chifukwa cha mphatso ya kukoma mtima imeneyi.” Kodi nchifukwa ninji anachita zinthu motere? Paulo akuyankha m’mavesi 20 ndi 21 mwa kusonyeza kuti timachepetsa mkhalidwe wa kukayikira abale kosayenera ngati ndalama zisoŵa.
◼ Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita ndi malisiti olembedwa pamene ndalama zitengedwa?
Kope lachiŵiri la lisiti losainidwa ndi abale aŵiri onsewo liyenera kuperekedwa kwa mlembi, ndipo lisiti loyamba pamodzi ndi ndalama zakezo ziyenera kuperekedwa kwa mtumiki wa maakaunti kuti zilembedwe ndi kusungidwa. Zimenezi ziyenera kuchitidwa ponse paŵiri potenga zopereka pa Nyumba Yaufumu ndi ku malo a Phunziro Labuku Lampingo. Kungakhale kothandiza ngati mbale amene amathandiza mtumiki wa maakaunti ali ndi emvulopu yokhala ndi dzina la mlembi imene angaikemo malisitiwo ndiyeno kuwapereka kwa mlembi pamene adzaonana naye.
◼ Kodi nkololedwa kwa munthu wosunga ndalama “kukongola” ndalama chifukwa cha zakugwa mwadzidzidzi? Kapena kodi kungakhale koyenera kulola wina aliyense “kukongola” ndalama chifukwa cha zakugwa mwadzidzidzi?
Ndalama zoperekedwazo nzampingo wonse. Palibe munthu amene amasankha za mmene ndalamazo ziyenera kugwiritsidwira ntchito. Pamene kuli kwakuti bungwe la akulu limayang’anira njira yogwiritsira ntchito ndalama zampingozo, pamene kugulidwa kwa kanthu kena kapadera kukufunika, akulu amapereka nkhaniyo kumpingo wonse kuti usankhe. Motero “kukongola” ndalama chifukwa cha zakugwa mwadzidzidzi ndiko kuba.—Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1994, masamba 19 ndi 20.
4 Kuthandiza kulipirira zowonongedwa za mpingo ndi kukhala ndi phande m’kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu kuli mwaŵidi. Komabe, sitikufuna konse kupemphetsa ndalama kwakuti abale amve kukhala akuumirizidwa, koma tikufuna kuti adziŵe bwino lomwe mmene mpingo umagwirira ntchito ndi mbali yawo pankhaniyi. Abale alinso ndi mwaŵi wa kuthandiza pantchito ya kupereka malo ndi chakudya kwa oyang’anira madera ndi azigawo panthaŵi ndi nthaŵi. Wonsewu ndi mwaŵi wa utumiki ndipo umafuna mzimu wa kufunitsitsa. Chotero tikhaletu ndi mbali m’kufutukula ntchito ya Ufumu m’gawo lathu lonse ndi zopereka zathu zaufulu ndiponso kutsimikizira kuti zolemba za maakaunti a mpingo zikusungidwa bwino. Motero tidzalemekeza Yehova ndi chuma chathu.