Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu November: Gaŵirani buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi pa mkupiti wapadera. Ngati mulibe, gaŵirani New World Translation ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? December: Knowledge That Leads to Everlasting Life. Yesetsani mwapadera kubwerera kumene munagaŵira mabukuwo, ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. January: Gaŵirani buku la Moyo wa Banja pa mkupiti wapadera. Chogaŵira china chingakhale buku lililonse la masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo m’sitoko. February: Buku la Moyo wa Banja pa mkupiti wapadera. Mipingo imene ilibe mtokoma wa mabuku ameneŵa ingagaŵire buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Awake! 1994; The Watchtower 1994 (baundi voliyamu)—Chifrenchi
Watch Tower Publications Index 1930-1985; 1991-1994—Chingelezi
◼ Makaseti Atsopano Avidiyo Omwe Alipo:
United by Divine Teaching—Chingelezi
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda 1996 Yearbook of Jehovah’s Witnesses paoda yawo ya mabuku ya November. (Onani Mpambo wa Mitengo ya Watch Tower, ndime 8.) Yearbook idzakhalapo m’Chingelezi. Kufikira pamene Yearbook idzakhalapo ndipo maoda apangidwa, idzasonyezedwa kuti “Zoyembekezeredwa” pamipambo yolongedzera katundu ya mipingo. Ma Yearbook ali zinthu za oda yapadera.
◼ Chonde dzazani silipi la M-202 pamene akaunti ya magazini yoipa yathetsedwa. Sosaite sidzangokutsegulirani akaunti ngati simudzaza masilipi ameneŵa. Podzaza masilipi ameneŵa, ŵerengani malangizo ake mosamala. Chiŵerengero choti mulembe pa silipi chiyenera kukhala chogwirizana ndi kope lililonse, osati cha mwezi wonse.