Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu February: Buku la Moyo wa Banja kaamba ka mkupiti wapadera. Mipingo imene ilibe mtokoma wa mabuku ameneŵa ingagaŵire buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa. March: Knowledge That Leads to Everlasting Life. April ndi May: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene siinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambazo iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Order (S-AB-14) ya mwezi ndi mwezi yotsatira.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki ayenera kupendanso ntchito za apainiya okhazikika onse. Ngati pali alionse amene ali ndi vuto la kufitsa maola ofunikira, akulu ayenera kulinganiza kupereka thandizo. Pendaninso nsonga m’ndime 12-20 za m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa October 1986.
◼ Phwando la Chikumbutso lidzakhalako pa Lachiŵiri, April 2, 1996. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumirirapo, chonde kumbukirani kuti kuyendetsa mkate wa Chikumbutso ndi vinyo si kuyenera kuyamba kufikira pambuyo pa kuloŵa kwa dzuŵa. Fufuzani kwa anthu a kumaloko kuti mudziŵe pamene dzuŵa limaloŵa kwanuko. Palibe misonkhano iliyonse imene iyenera kuchitidwa patsikulo kusiyapo yokonzekera utumiki wakumunda. Ngati nthaŵi zonse mpingo wanu umakhala ndi misonkhano pa Lachiŵiri, mungaisinthire ku tsiku lina la mlungu umenewo ngati Nyumba Yaufumu idzakhala isakugwira ntchito.
◼ Ofalitsa amene akufuna kutumikira monga apainiya othandiza mu March, April, ndi May ayenera kukonzekera tsopano ndi kupereka zofunsira zawo mwamsanga. Zimenezi zidzathandiza akulu kupanga makonzedwe oyenera a utumiki wakumunda ndi kukhala ndi magazini ndi mabuku ena pafupi.
◼ Zofalitsa Zimene Zilipo:
Knowledge That Leads to Everlasting Life.—Chifrenchi
Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza,—Chicheŵa, Chingelezi
◼ Ma Vidiyokaseti Atsopano Amene Alipo:
To the Ends of the Earth (mbiri yazaka 50 ya Sukulu ya Gileadi)—Chingelezi