Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndime ziyenera kuŵerengedwa motani paphunziro la buku lampingo ndi paphunziro la Nsanja ya Olonda?
Kaŵirikaŵiri timaŵerenga ndi kukambitsirana ndime imodzi panthaŵi imodzi. Komabe, ngati funso liphatikiza pamodzi ndime ziŵiri kapena zitatu, woŵerenga adzaŵerenga ndimezo pamodzi. Zitaŵerengedwa, wochititsa amaŵerenga funso ndi kupatsa mwaŵi omwe anyamula manja kuti ayankhe. Pambuyo pake apempha woŵerenga kuti aŵerenge ndime yotsatira. Sibwino kuŵerenga ndime zingapo panthaŵi imodzi mmene mipingo ina imachitira.
Woŵerenga sayenera kutchula malemba osonyezedwa m’mabulaketi kapena kumapeto kwa ndime. Ameneŵa angoikidwamo kuti achirikize malingaliro a Malemba m’ndimezo ndipo onse akulimbikitsidwa kuwaŵerenga pokonzekera phunzirolo. Mawu amtsinde opereka malongosoledwe owonjezereka ku ndimeyo ayenera kuŵerengedwa, koma ngati angotchula za chofalitsa chosindikizidwa ndi Sosaite kapena gulu lina, sikofunikira kuwaŵerenga.
Chifuno cha kuŵerenga ndime pamisonkhano ndicho kupindulitsa mwauzimu awo opezekapo. Chifukwa chake, pafunikira kukonzekera bwino kuti kuŵerenga pamisonkhano kukhale kwabwino ndi kwa myaa. Pamene munthu aŵerenga pang’onopang’ono kwambiri, kungakhale kovuta kuti wochititsa amalize phunziro panthaŵi yake. Kugogomezera mawu kolakwika, kusatchula bwino mawu ndi kubwerezabwereza mawu kungakhale kosokoneza ndi kododometsa abale ndi okondwerera amene akuyesayesa kusumika maganizo pankhaniyo. Kuŵerenga kwapoyera kuyenera kukhala kosadodoma. (Aheb. 2:2) Popeza kuti chifuno cha kuŵerenga kwapoyera ndicho kuphunzitsa ena, woŵerenga poyera ayenera kumvetsa bwino lomwe zimene akuŵerenga ndi kuzindikira chifuno cha wolemba nkhaniyo, akumasamala poŵerenga kuti apeŵe kupereka lingaliro kapena tanthauzo lolakwa kwa omvetsera. Malinga ndi kunena kwa Chivumbulutso 1:3, awo amene amaŵerenga ulosiwo momveka, limodzi ndi awo akumva mawuwo ndi kuwasunga, adzakhala achimwemwe.
Pa zifukwa zimenezi, awo opatsidwa mbali za kuŵerenga pamisonkhano yampingo ayenera kukumbukira mawu a mtumwi Paulo pa 1 Timoteo 4:13 akuti: “Usamalire kuŵerenga, kuchenjeza, kulangiza.”