Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/97 tsamba 1
  • Loyamba m’Malaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Loyamba m’Malaŵi
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 5/97 tsamba 1

Loyamba m’Malaŵi

1 Mwezi uno wa May ngwapadera muno m’Malaŵi. Kwa nthaŵi yoyamba, tidzakhala tikufalitsa brosha limodzimodzi m’zinenero zinayi. Paja mukudziŵa kale kuti brosha lamutu wakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? linatulutsidwa m’Chicheŵa ndi m’Chingelezi pamisonkhano yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu.” Tsopano tili okondwa kulengeza kuti brosha limeneli latulukanso m’Chitumbuka ndi m’Chiyao. Tasangalala kwambiri chifukwa chofalitsa chimenechi nchoyamba kupezeka m’Chitumbuka kuyambira pamene ntchito yathu inaletsedwa zaka ngati 30 zapitazo. M’Chiyao, limeneli ndi brosha loyamba limene Sosaite yasindikiza. Chinthu china chimene ofalitsa athu achiyao analandira linali trakiti lakuti Moyo pa Dziko Lapansi basi, zaka ngati 30 zapitazo.

2 Kodi nchifukwa ninji May ati akhale wapadera kwa ife? Tidzakhala tikugaŵira brosha la Mulungu Amafunanji monga mkupiti wapadera. Zinenero zake zidzakhala Chicheŵa, Chingelezi, Chitumbuka, ndi Chiyao. Kuti ithandize mipingo, Sosaite idzakhala ikutumizira mpingo uliwonse mitokoma ya mabroshawo m’zinenero zimene mipingoyo imalankhula. Zimenezi zikutanthauza kuti mpingo uliwonse udzakhala nawo kuti uwagaŵe. Chotero tikulimbikitsa mipingo kuti iwagwiritsire ntchito ndiponso kutengamo mbali mokangalika m’kuwagaŵa. Mwa njira imeneyi, uthenga wabwino udzafalitsidwa kwa anthu m’zinenero zawo. Malinga ndi kunena kwa Yesu: ‘Uthenga Wabwino udzalalikidwa kwa anthu amitundu yonse,’ ndiponso m’Chivumbulutso, mngelo wouluka pakati pa mlengalenga anali ndi ‘uthenga wabwino, aulalikire kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe.’—Mat. 24:14; Chiv. 14:6.

3 Limodzi ndi mtokoma uliwonse padzakhala fomu yapadera. Idzasonyeza chiŵerengero cha mabrosha amene tatumiza ndi kukupemphani kulemba chiŵerengero chimene ofalitsa ndi apainiya atenga. Mudzaze makope aŵiri a fomuyo. Pamene galimoto ya Sosaite ifika pamalo otula katundu wa mpingo wanu mwezi wamaŵa, tingakonde kulandira fomu yolembalemba, ndiponso ndalama zokwanira za mabrosha amene mwagaŵira.

4 Ngati mabrosha atha pampingo panu, chonde musazengereze kuodetsa ena. Ngakhale mipingo imene maakaunti ake sali bwino tidzaitumizira makope ena mwa makonzedwe amene talongosolawa.

5 Tikuyamika Yehova kuti wapereka chothandizira kuphunzira m’zinenero zina ziŵiri za m’Malaŵi. Pamene mukugwiritsira ntchito zofalitsa zimenezi, tikutsimikiza kuti anthu ambiri adzakopeka ndi choonadi. M’May tikufuna kungolimbikira kugaŵa brosha la Mulungu Amafunanji. Kenako, tikulimbikitsa nonse kubwerera kumene munasiya brosha ndi kuyesa kuyamba maphunziro a Baibulo ambiri. “Loyamba m’Malaŵi” limeneli liyendetu bwino pamene nonse mukutengamo mbali mumkupiti wa dziko lonse lino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena