Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/98 tsamba 3-4
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 1/98 tsamba 3-4

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1985 isanafike lomwe mpingo uli nalo m’sitoko. Mipingo yomwe ilibe mabuku amenewo ingagaŵire brosha lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” February: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wasatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

◼ Ofalitsa onse obatizidwa omwe adzapezeka pa Msonkhano Wautumiki mlungu woyambira January 5 adzalandira khadi la Advance Medical Directive/Release ndi ma Identity Card a ana awo.

◼ Nthaŵi iliyonse kuyambira m’February mpaka March 1, oyang’anira madera adzayamba kukamba nkhani yawo yatsopano yakuti “Kodi Mumaona Moyo Monga Mmene Mulungu Amauonera?”

◼ Mipingo iyenera kupanga makonzedwe oyenera a phwando la Chikumbutso chaka chino Loŵeruka, pa April 11, dzuŵa litangoloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe msanga, zizindikiro za Chikumbutso musayambe kuziyendetsa mpaka dzuŵa litaloŵadi. Funsirani kwa odziŵa za nyengo kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi imene dzuŵa limaloŵa kwanuko. Ngakhale kuti mpingo uliwonse ungakonde kuchita phwando la Chikumbutso lawolawo, nthaŵi zina zimenezo sizingatheke. Ngati mipingo ingapo imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzimodziyo, mwina mpingo umodzi kapena ingapo ingabwereke nyumba ina yogwiritsira ntchito madzulowo. Chikumbutso chisayambike mochedwa kwambiri kuti anthu okondwerera chatsopano asavutikire kupezekapo. Programuyo isakhale yopanikiza kwambiri moti nkusoŵeratu nthaŵi yolonjera alendo phwandolo lisanayambe kapena pambuyo pake. Nthaŵiyo imakhala yofunika kuti mupange makonzedwe akupitiriza kupereka chithandizo chauzimu kwa okondwerera, kapena kukhala ndi macheza olimbikitsana ndi ena. Akulu atalingalira zinthu zonse, ayenera kukonza zinthu mwa njira imene idzathandiza onse opezekapo pa Chikumbutso kupindula kwambiri ndi chochitikacho.

◼ Nkhani yapoyera ya nyengo ya Chikumbutso cha 1998 idzakambidwa Lamlungu, pa March 29. Autilaini yake tidzakutumizirani. Mipingo yomwe ikuchezeredwa ndi woyang’anira dera, yomwe ili ndi msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera idzakhala ndi nkhani yapaderayo mlungu wotsatira. Pasakhale mpingo wina umene udzakhala ndi nkhani yapaderayo March 29, 1998 isanafike

◼ Bungwe la akulu lizidziŵa kuti liyenera kusintha zina ndi zina zonga zotsatirazi, pamene mipingo ya kwawo ili ndi misonkhano yadera: Ngati pati padzakhale programu ya tsiku la msonkhano wapadera, mpingo ungachite misonkhano yonse yanthaŵi zonse mlungu wonsewo, kupatulapo Msonkhano Wapoyera ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda ndizo zingalephereke. Ngati mpingo uti udzakhale ndi msonkhano wadera, udzalepheranso kuchita Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Msonkhano Wautumiki; koma ungachite Phunziro Labuku Lampingo basi kwawoko mlungu umenewo.

◼ Tikukumbutsa ofalitsa onse kuti mabuku onse a masamba 192 omwe anafalitsidwa 1985 isanafike, kupatulapo buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona, la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, ndi lakuti Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, atsitsidwa mtengo mpaka pa 40 tambala. Buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona nalo latsitsidwa mtengo mpaka pa K6.00 kope lililonse kwa wofalitsa, ndipo K1.50 kope lililonse kwa mpainiya aliyense. Buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu lili pa K6.00 kwa ofalitsa ndi apainiya omwe. Ngati ofalitsa agaŵira mabuku a masamba 192 ameneŵa, mlembi ayenera kuona kuti wasonyeza zimenezo pa fomu ya S-20.

◼ Kuchokera pa mlungu woyambira May 4, 1998, mpaka mlungu woyambira September 14, 1998, buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona lidzaphunziridwa pa Phunziro la Buku la Mpingo.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja—Chicheŵa, Chingelezi

Revelation—Its Grand Climax at Hand—Chingelezi

Watchtower Publications Index 1996—Chingelezi

◼ Makaseti Omwe Alipo (m’Chingelezi basi):

Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo (makaseti anayi mu alabamu imodzi)

Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha (makaseti asanu mu alabamu imodzi)

Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja (makaseti anayi mu alabamu imodzi)

Imbirani Yehova Zitamando (makaseti asanu ndi atatu mu alabamu imodzi)

Kingdom Melodies (makaseti asanu ndi atatu mu alabamu imodzi)

Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo (makaseti anayi ndi buku mu alabamu imodzi)

Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako (makaseti asanu ndi atatu mu alabamu imodzi)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena