Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/98 tsamba 7
  • “Yehova Ndiye Mthandizi Wanga”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Yehova Ndiye Mthandizi Wanga”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndapanga Mzimu Woyera Kukhala Mthandizi Wanga?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kulimba Mtima Kwambiri Chifukwa cha Chikondi
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Khalani Olimba Mtima!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • ‘Khalani Amphamvu Ndipo Limbikani Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 2/98 tsamba 7

“Yehova Ndiye Mthandizi Wanga”

1 Potumiza ophunzira ake, Yesu anawauza kuti: “Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi.” (Mateyu 10:16) Kodi mawu amenewo anawachititsa mantha nkuleka kupita? Iyayi. Iwo analimba mtima monga mmene mtumwi Paulo panthaŵi ina anadzauzira Akristu anzake kuti: “Limbani mtima nimuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzaopa. Adzandichitira chiyani munthu?’” (Aheb. 13:6, NW). Iwo anakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu, ndipo sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira uthenga wabwino.—Mac. 5:41, 42.

2 Lerolino ntchito yolalikira padziko lonse yatsala pang’ono kutha. Monga momwe Yesu ananeneratu, mitundu yonse imatida kumene. (Mat. 24:9) Ntchito yathu yolalikira imatsutsidwa ndi kunyozedwa, ndipo kumbali zina za dziko lapansi, anangoiletseratu. Ngati tinali opanda chikhulupiriro, tikanachita mantha. Komabe, kudziŵa kuti Yehova ndiye Mthandizi wathu kumatitsitsimula ndipo kumatilimbikitsa kuti tipirire.

3 Kulimba mtima ndiwo mkhalidwe wa kupanda mantha, kulimbika. Nkosiyana ndi mantha. Ophunzira a Yesu nthaŵi zonse akhala akufunikira kulimba mtima kuti apirire. Kulimba mtima nkofunika kuti tisalefulidwe ndi mzimu wa dzikoli ndi zochita za dzikoli lokhala paudani ndi Mulungu. Nkolimbikitsa chotani nanga kuganiza za chitsanzo chopambana cha Yesu, yemwe analaka dzikoyo! (Yoh. 16:33) Kumbukiraninso atumwi, kuti pamene anali m’ziyeso zazikulu, ananena molimba mtima kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Mac. 5:29.

4 Ife Si Ndife a Iwo Akubwerera: Tiyenera kuyesetsa kusalema nayo ntchito yathu. (Aheb. 10:39) Nthaŵi zonse tizikumbukira kuti Yehova akutitumiza kwa anthu onse monga njira yosonyezera chikondi ndi chifundo chake. Iye samapempha atumiki ake kuchita chilichonse chomwe chili chosapindulitsa. Chilichonse chimene watipatsa kuti tichite potsirizira pake chidzakhala chopindulitsa awo amene amakonda Mulungu.—Aroma 8:28.

5 Kukhulupirira kuti zinthu ziyenda bwino basi kuzititheketsa kufunafuna anthu onga nkhosa m’gawo lathu. Anthu osonyeza mphwayi tiziwaona monga ngati kuti akusonyeza kupanda kwawo chiyembekezo. Chikondi chathu chizitisonkhezera kuwamvera chifundo ndi kuleza nawo mtima. Tikagaŵira buku kapena mwina taona ngati wina wachita chidwi, cholinga chathu chizikhala chobwererako msanga kuti tikakulitse chidwicho. Tisamakayikire konse kuti sitingathe kuyambitsa phunziro la Baibulo kapena kuti mwina sitingaphunzitse bwino. Koma nthaŵi zonse tizipemphera kwa Yehova kuti atithandize ndi kutitsogoza, tikumadalira kuti atithandizadi.

6 Tikukhulupiriradi kuti Yehova adzaiyang’anira ntchitoyi mpaka tiitsirize. (Yerekezerani ndi Afilipi 1:6.) Kumdalira kwathu kosakayikira monga Mthandizi wathu kumatilimbikitsa, choncho ‘sitilema pakuchita zabwino.’—Agal. 6:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena